Mwana wa njovu wachidwi
Judith Baker
Wiehan de Jager

Aliyense amadziwa kuti njovu ili ndi mphuno yaitali.

1

Koma kalekale, mphuno ya njovu inali yayifupi komanso yonenepa.

Imaoneka ngati nsapato pakati pa nkhope.

2

Tsiku lina kunabadwa mwana wa njovu. Amachita chidwi ndi chilichonse.

Amakhala ndi funso kwa nyama ina iliyonse.

3

Anachita chidwi ndi Kadyamsonga.

"Ndi chifukwa chiyani uli ndi khosi lalitali?" anafunsa.

4

Anachidwa chidwi ndi chipembere.

"Ndichifukwa chiyani nyanga yako ili yosongoka?"

5

Anachidwa chidwi ndi mvuu.

"Ndichifukwa chiyani maso ako ndi ofiira?"

6

Anachita chidwi chachikulu ndi ng'ona.

"Kodi ng'ona zimadya chiyani madzulo?" anafunsa.

7

"Osadzafunsanso funso ngati limenero!" mayi ake anamuuza.

Kenako ananyamuka atakwiya.

8

Mwachangu! Khwangwala anawulukira kwa mwana wa njovu uja.

"Nditsatire kumtsinje. Kumeneko ukaona chimene Ng'ona imadya madzulo," anatero khwangwala.

9

Kotero, mwana wa njovu uja anatsatira khwangwala kupita ku mtsinje.

10

Anawanda mabango ndikuima m'mbali mwa mtsinje.

Anayang'ana m'madzi. Ng'ona ali kuti?

11

"Moni," unatero mwala umene unali m'mbali mwa mtsinje.

"Zikomo," anayankha mwana wa njovu. "Ungandiuze kuti Ng'ona imadya chiyani madzulo?" anafunsa.

12

"Werama ndikuuza," unatero mwala uja. "Werama kwambiri," unanena mwala uja.

Kotero mwana wa Njovu uja anaweramira mumtsinje muja kwambiri.

13

Gwii! Mwadzidzi mphuno ya mwana wa njovu inagwidwa ndi ng'ona.

"Ng'ona ikudya ngati chakudya cha madzulo!" anakuwa khwangwala, kenako anawulukira kutali.

14

Mwana wa njovu anakhalira zimiyendo zake zakumbuyo. Anakoka ndi kukoka.

Koma Ng'ona sanaisiye mphuno ya mwana wa njovu.

15

Mphuno ya mwana wa njovu inakokeka ndi kukokeka kwambiri.

Kenako, "Phuuu!" Mwana wa njovu anagwa chagada.

16

Ng'ona ija inagwera m'madzi kuti phavaa!

Anakhumudwa kuti anataya chakudya chake cha madzulo.

17

Mwana wa njovu anaona mphuno yake.

Inatamuka kwambiri. Samathanso kuona kumene yathera.

18

Mphuno yake inali yaitali kwambiri, amatha kutsitsa zipatso kuchoka m'nthambi za m'mwamba kwambiri.

19

Mphuno yake inali yaitali kwambiri amatha kudzikapiza madzi ku msana.

Kuchoka tsiku limenelo, njovu zonse zimakhala ndi zitamba zitalizitali komanso za phindu.

20
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mwana wa njovu wachidwi
Author - Judith Baker, Lorato Trok
Translation - Peter Msaka
Illustration - Wiehan de Jager
Language - ChiChewa
Level - First sentences