Mwana wamkazi wokondedwa
Ritah Katetemera
Brian Wambi

Uyu ndi Natabo.

Ali ndi achimwene ake sikisi.

1

Makolo ake amupatsa kam'phika kakang'ono.

Amaukonda m'phikawu.

2

Tsiku lina mchimwene wake aswa m'phikawo.

3

Natabo sakuupeza m'phika wake.

Alira kosalekeza.

4

Natabo athawa.

Akwera mtengo wautali kwambiri.

5

Makolo ake amupeza.

"Chonde tsika," amupempha.

6

Achimwene ake aja ayimba nyimbo, "Chonde tsika."

7

Natabo aseka mayimbidwe a nyimboyo.

8

Kenako, mzake wa Natabo afika.

"Chonde tsika," ayimba motero.

9

Mzake wa Natabo ayimba mpaka Natabo atsika mumtengo muja.

10

Onse ayenda kupita kunyumba.

11

Onse asangalala kuti Natabo wabwera kunyumba.

Natabo amupatsa mphika wina.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mwana wamkazi wokondedwa
Author - Ritah Katetemera, Mulongo Bukheye
Translation - Peter Msaka
Illustration - Brian Wambi
Language - ChiChewa
Level - First sentences