Ndi mutu wanga ndimaganiza.
Ndi maso anga, ndimaona zinthu.
Ndi mphuno zanga ndimamva fungo.
Ndi kamwa langa ndimadya.
Ndi lilime langa ndimamva kukoma kapena kuwawa.
Ndi khungu langa ndimamva kuzizira kapena kutentha.
Ndi manja anga ndimanyamula zinthu.
Ndi miyendo yanga ndimayenda.