Bingu ndi Mphenzi
Ogot Owino
Jesse Breytenbach

Kalekale, Bingu ndi Mphenzi zimakhala pa dziko lapansi limodzi ndi anthu.

1

Bingu anali mayi wa Mphenzi.

2

Mphenzi anali wokwiya msanga ndipo kawilikawili amakangana ndi ena.

3

Nthawi zonse Mphenzi akakwiya amanka akuyatsa nyumba ndi kugwetsa mitengo.

Amachita phokoso loopsa, "Pha-pha-la-la-la, pha-pha-la-la-la!"

Amawononga minda, komanso amatha kupha anthu.

4

Nthawi zonse Mphenzi akachita zimenezi, amayi ake amamuitana ndi mawu okuwa kwambiri, "Phomu! Gu-gu-lu-lu-lu, Phomu!"

Amayesetsa kumuletsa kuononga zinthu.

5

Koma Mphenzi samalabada za zimene mayi ake amanena.

Amasowetsa mtendere aliyense akakwiya.

6

Zinafika poti anthu anakadandaula kwa amfumu.

7

Amfumu analamula kuti Bingu ndi mwana wake achoke m'mudzi muja.

Anawathamangitsira kutali ndi nyumba za anthu.

8

Izi sizinathandize kwenikweni. Mphenzi akakwiya amatenthabe nkhalango, "Pha-pha-la-la-la, pha-pha-la-la-la!"

Malawi amoto nthawi zina amayambukira kuminda ndi kuyambitsa moto wowononga.

9

Kotero, anthu anakadandaulanso kwa amfumu.

10

Tsopano, amfumu analamula Mphenzi ndi Bingu kuti asakhalenso padziko la pansi.

Anawalamula kuti azikakhala mlengalenga, kumene sakanaononganso zinthu kwambiri.

11

Kuchokera nthawi imeneyo, Mphenzi akakwiya, amatha kutentha ndi kuwononga zinthu, "Pha-pha-la-la-la, pha-pha-la-la-la!"

Komanso timamvanso mayi ake, Bingu, akumukalipira, "Phomu! Gu-gu-lu-lu-lu, Phomu!"

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Bingu ndi Mphenzi
Author - Ogot Owino
Translation - Peter Msaka
Illustration - Jesse Breytenbach
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs