Chitsanzo, dilaiva wamkazi
Dawit Girma
Yirgalem Birhanu

Njingalimoto ndi galimoto ya matayala atatu.

Imagwiritsidwa ntchito mtawuni kuti anthu ayende mwachangu kupita malo osiyanasiyana.

1

Mdera lathu, kuyendetsa galimoto ndi ntchito ya amuna.

Akazi sagwira ntchito imeneyi.

2

Tsiku lina, Abebech anapempha makolo ake kuti amupatse ndalama zokaphunzirira kuyendetsa galimoto.

Makolo ake anati, "Ntchito imeneyi siyabwino kwa atsikana. Anthu aziti chiyani?"

3

Komabe, Abebech anati, "Ndili ndi kuthekera kochita chilichonse chimene anthu ena angathe." Anakwanitsa kuwanyengerera makolo ake.

Makolo ake anavomera kuti akayambe kuphunzira kuyendetsa galimoto.

4

Abebech anamaliza ndi kukhonza maphunziro aja.

Makolo ake anakambirana zoti achite kutsatira maphunziro ake.

5

Pamapeto pake, anagwirizana zomugulira njingalimoto.

Kotero, Abebech anayamba kuyendetsa njingalimoto m'misewu ya mumzinda wa Debre Birhan.

6

Tsiku lina Abebech anaganiza mwakuya.

Anamata uthenga ndi nambala yake ya foni kumbuyo kwa njingalimoto yake.

7

Uthengawo unati, "Ndimanyamula ulele amayi oyembekezera, amayi amene abereka kumene, komanso ana ang'ono."

Amayi onse amene ana awo adwala amamuimbira Abebech.

8

Abebech anapanga ndalama zambiri ponyamula anthu.

Anapitiliza kunyamula ulele anthu amene analibe ndalama.

9

Abebech anali okondwa kwambiri ndi ntchito yake. Anthu okalamba anamudalitsa. Aliyense amakamba za iye nthawi zonse.

Abebech anawauza kuti, "Kuchita zabwino kumadalitsa."

10
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Chitsanzo, dilaiva wamkazi
Author - Dawit Girma
Translation - Peter Msaka
Illustration - Yirgalem Birhanu
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs