Anzanga
Zimbili Dlamini
Catherine Groenewald

Dzina langa ndine Simo.

1

Ndine wokondwera kwambiri kukhala ndi nthawi yokuuzani nkhani pakati pa anzanga.

2

Ndili ndi anzanga okwanira anayi ndipo maina awo ndi awa: Woyamba ndi Zizo, waciwiri ndi Lele, wacitatu ndi Sisa ndipo wotsirizira ndi Ayanda.

3

Monga mmene mudziwira kuti munthu aliyense ali ndi cinthu cimene amakonda kucita.

Zizo amakonda kambili kuchaya bola.

4

Lele ndi mnyamata amene amamvera bwino kusambira m'madzi.

5

Sisa amakonda kwambili masewera a kabisabisa.

Masowera awa amacitika nthawi yausiku paja kuli mwezi.

6

Ayanda amakonda kwambiri kuwerenga mabuku.

7

Ndidziwa mui mtima mwanu mukufunsa kuti, "Nanga ine ndimakonda kwambiri masewera otani?" M'masewera a mpira ndimapezeka. M'masewera osambira ndipezeka.

Kabisabisa ndimacita, mpira ndimachaya. Kapena kuwerenga, ndimawerenga.

8

Ine kulibe kumene ndimapezeka kwenikweni.

Cifukwa ndikapezeka ndi Zizo, nimamenya mpira.

9

Ngati ndili ndi Lele, ndimasambira m'madzi.

10

Ngati Sisa wabwera, ndimacita kabisabisa.

11

Mnzanga waitanidwa, nanga iwe, ndimasewera otani amene umakonda kwambiri?

12

Bwera tichaye mpira.

13

Bwera tisambire pamadzi.

14

Bwera ticite kabisabisa.

15

Bwera tiwerengere pamodzi.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Anzanga
Author - Zimbili Dlamini, Hlengiwe Zondi
Adaptation - Bether Mwale-Moyo
Illustration - Catherine Groenewald
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs