Shupiwe wolankhula kwambiri
Gaspah Juma
Jesse Breytenbach

Kalekale, panali mtsikana wina wochedwa kuti Shupiwe. Mtsikana ameneyu anali wokambakamba kwambiri.

Ngakhale kuti amai ake anamucenjeza kuti asadzikamba kwambiri, koma iye sanamvere.

1

Amai ake aang'ono amakhala patsidya lina la mudzi wawo.

Tsiku lina, amai ake aang'ono amenewo anadwala. Panalibe aliyense wowasamalira.

2

Amayi ake Shupiwe anali wotangwanika kwambiri.

Inali nthawi ya m'madzulo pamene iwo anapatsa Shupiwe cakudya cakuti apereke kwa amai ake aang'ono wodwala.

3

Pa njira, Shupiwe anakumana ndi Sinson.

Iyeyu anali fisi amene anadzisintha kukhala munthu.

4

Sinson anafunsa Shupiwe, "Kodi mwanyamula ciyani umo?"

Shupiwe anayankha, "Ndanyamula nyama, mazira ndi mkaka."

Amai ake kunyumba anali atamucenjeza kuti asauze aliyense cimene wanyamula.

5

Shupiwe ananenanso kuti, "Ndikupita kukaona amai anga aang'ono, wodwala."

Sinson ananyambita milomo yake poganizira za nyama imene Shupiwe ananyamula.

6

Fisi uja anathamangira kutsogolo kunyumba ya amai ake aang'ono a Shupiwe.

7

Iye anadya amai ake aang'ono a Shupiwe ndipo pambuyo pake anafunda bulangete yawo.

8

Pamene Shupiwe anafika, kunyumba kuja kunali zii.

Iye analowa m'kati ndi kuitana, "Amai aang'ono muli kuti?"

9

Shupiwe sanamvere liu la amai ake aang'ono. Anlowa mcipinda cam'kati momwe iwo amagona.

Atafika pafupi anadabwa pamene anaona munthu wofunda bulangete.

10

Iye anafunsa nati, "Amayi anga n'cifukwa ciyani makutu anu akula kwambiri lero?"

Fisi, Sinson anayankha, "Kuti nikazikumvesesa bwino."

11

Shupiwe anafunsanso, "Amai, n'cifukwa ciyani maso anu akula kwambiri lero?"

Sinson anayankha, "Kotero kuti ndizikuona bwino."

12

Shupiwe anafunsanso, "Amai, n'cifukwa ciyani mlomo wanu wakula tere lero?"

Sinson anayankha, "Kotero kuti ndikudye bwino!" Pamenepo iye analumpha kucoka mu bedi ndipo anadya Shupiwe.

13

Shupiwe anapitiriza kulankhula ngakhale pamene anali m'mimba mwa Sinson, fisi.

Iye anafunsa mafunso ambiri.

14

Pomalizira pake, Sinson analema ndi mafunso ambiri a Shupiwe ndipo anaganiza zomulavula.

15

Antu a mumunzi anatandiza Shupiwe na amai ake ang'ono.

Kucokela apo, Shupiwe analeka kukambisa antu amene saziba bwino bwino.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Shupiwe wolankhula kwambiri
Author - Gaspah Juma
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Jesse Breytenbach
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs