Kulemala sikulephera kucita zinthu
Agnes Mabururu
Wiehan de Jager

Awa ndi a Agnes.

Ndi aphunzitsi anga.

1

A Agnes amagwiritsa nchito ndodo poyenda.

2

Uyu ndi Metobo.

Iwo ndi a DJ a pawailesi anga a pamtima.

3

Metobo ali ndi vuto la maso.

4

Uyu ndi Moraa, amene timakhala naye pafupi.

Moraa ndi mlimi.

5

Moraa ndi gonthi.

Iye amagwiritsa nchito cilankhulo ca manja.

6

Uyu ndi Osera.

Iye ndi munthu wochuka wa masewero a mpira pa sukulu lathu.

7

Osera alibe manja, koma agolesa kwambili mu gulu latu la a mpira.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kulemala sikulephera kucita zinthu
Author - Agnes Mabururu
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - First sentences