Ng'ombe ya nyanga imodzi
Sebongile Daniel
Marion Drew

Eh, eh, eh!

Kuli ng'ombe yokongola kunyumba.

1

Ng'ombe imeneyi ili ndi nyanga imodzi cabe, ndiponso ilibe mcira.

2

Ng'ombe imeneyi ndi yonenepa, ndipo ili ndi cifu cacikulu.

3

Imeneyi ndi ng'ombe yamphamvu.

4

M'busa amaikonda ng'ombe imeneyi.

5

Pamene ng'ombe zina zikudya udzu, ng'ombe imeneyi imadya payokha.

6

Ng'ombe imeneyi ndi ya nkhondo.

Ng'ombe zinazonse zimayisiya yokha.

7

Kuti ukumane na ng'ombe yotele, ungacite cani?

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Ng'ombe ya nyanga imodzi
Author - Sebongile Daniel, Mpho Ntlhanngoe, Khothatso Ranoosi
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Marion Drew
Language - CiNyanja
Level - First words