Ganizani ndi Poto Wakufa
Peter Kisakye
Emily Berg

Kalekale, panali munthu wina dzina lake Ganizani, amene anali ndi ng'ombe imodzi. Tsiku lililonse, Ganizani amadyetsa ng'ombe yake.

Iye amaipatsanso madzi akumwa, koma iye anali cabe ndi kapoto kakang'ono kamadzi.

1

Conco, iye anapita kunyumba kwa aneba ake kuti abwerekeko poto waukulu wa madzi.

Aneba ake anvomera kumubwereka mbiya ya madzi, nati, "Vuto la neba wanga ndi vuto langanso."

2

Patapita masiku ocepa, Ganizani anapita kwa woumba mbiya, nagula kapoto kakang'ono. Anapita nako kunyumba.

Anakakaika m'kati mwa poto waukulu umene anabwereka uja kwa aneba ake.

3

Pambuyo pake, iye anaika poto waung'ono m'kati mwa poto waukulu, nausenza pamutu pake.

Anabweza poto wakulu uja anabwereka kwa mnzake.

4

Ganizani anamuuza mnzake kuti, "Ndabweretsa poto uja ndinabwereka, wabereka poto unzake."

Neba wake uja anadabwa kwambiri kuti poto wake wabereka poto wina. Anamuyamikira Ganizani kuti, "Banja lako ndi lodalitsika."

5

Patapita masiku ocepa, Ganizani anapitanso kwa neba wake uja ndi kubwerekanso poto waukulu uja.

Iye analibe zolinga zabwino.

6

Mwini wapoto waukulu anayembekezera mosangalala kuti Ganizani abweze poto wake.

Potsirizira pake, iye analondola Ganizani kunyumba kwake nati, "Ndabwera kudzatenga poto wanga."

7

Ganizani anauza neba wake kuti, "Mnzanga, poto wako uja unafa. Pano, ndinali kukonzekera kubwera kwanu kuti ndikuuze za nkhani yacisoni imeneyi."

8

Mnzake uja anawomba m'manja modabwa. Nkhope yake inasintha ndi mkwiyo.

Anamukalipira Ganizani, "Sindinamvepo za poto kufa!"

9

Ganizani anayankha nati, "Mnzanga, uyenera kuvomera zinthu izi. Cinthu ciliconse cimene cimabereka ciyenera kufa. Nanenso ndinali ndi cisoni ndi imfa ya poto waukulu."

10

Mnzake anakwiya kwambiri ndipo anapita kubwalo lamilandu kumphala. Amfumu anamvetsera ku madandaulo a awirirwo.

Iwo anapeza kuti mwini wa poto anali wolakwa ndipo anaweruza kuti Ganizani akasunge poto wakufawo.

11

"Pamene Ganizani anakuuza kuti poto inabereka, unavomera. Pamene iye akuti ciliconse cimene cimabereka ciyenera kufa, iye ananena zoona."

Umu ndi mmene woweruza anaweruzira mlandu.

12

Mnzake wa Ganizani anapita kunyumba ngati nkhono.

Ganizani anatenga poto kamba kakuchenjela kwake.

13
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Ganizani ndi Poto Wakufa
Author - Peter Kisakye
Adaptation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Emily Berg
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs