Kalabushe wobwetuka
Gaspah Juma
Jesse Breytenbach

Kalekale, kunali mtsikana wina dzina lake Kalabushe.

Kalabushe anali mtsikana wokonda kuyankhula kwambiri. Ngakhale mayi ake anamuchenjeza kuti asamayankhule kwambiri, Kalabushe sanamvere.

1

Azakhali a Kalabushe amakhala mudzi umene unali mbali ina ya chigwa.

Tsiku lina azakhaliwo anadwala. Panalibe oti angawasamale.

2

Mayi a Kalabushe anali wotanganidwa kwambiri.

Kotero anali madzulo kwambiri pamene anamupatsira Kalabushe chakudya kuti akawapatsire azakhali ake.

3

Panjira, Kalabushe anakumana ndi Sinson.

Sinson anali fisi amene anasunduka kukhala munthu.

4

Sinson anamufunsa Kalabushe, "Wanyamula chiyani?" Kalabushe anayankha, "Ndanyamula nyama, mazira ndi mkaka."

Koma mayi ake anamuchenjeza kuti asauze aliyense chimene wanyamula.

5

Kalabushe anapitiliza kunena kuti "Ndikukapereka chakudyachi kwa azakhali anga amene akudwala."

Sinson ananyambitira milomo yake poganizira za nyama imene Kalabushe ananyamula.

6

Mwachangu Sinson anathamangira kutsogolo, kupita kunyumba kwa azakhali a Kalabushe.

7

Sinson anawameza azakhali a Kalabushe, ndikudzifundika gombeza lawo.

8

Kalabushe atafika, kunyumbako kunali zii.

Analowa m'nyumbamo naitana, "Azakhali, muli kuti?"

9

Kalabushe sanamve mawu a azakhali ake aja. Analowa ku chipinda chimene azakhali ake amagona.

Anadabwa ataona munthu atadzifundika chigombeza chachikulu.

10

Kalabushe anafunsa, "Azakhali, kodi bwanji makutu anu akuoneka akulu zedi lero?"

Sinson anayankha kuchokera m'gombeza muja, "Kuti ndizikumva bwino bwino."

11

Kalabushe anafunsanso, "Azakhali, ndi chifukwa chiyani maso anu akuoneka akulu lero?"

Sinson anayankhanso, "Kuti ndizikuona bwino bwino."

12

Kalabushe anafunsaso, "Azakhali, bwanji kukamwa kwanu kukuoneka kwakukulu lero?"

Sinson anayankha, "Kuti ndikumeze iweyo!" Sinson anadumpha pa bedi ndikum'meza Kalabushe.

13

Kalabushe sanasiye kuyankhula ngakhale anali m'mimba mwa Sinson. Anafunsa mafunso ambirimbiri.

14

Pamapeto pake, Sinson anatopa ndi mafunso amene Kalabushe amafunsa moti anaganiza zongomulavula.

15

Kalabushe ndi azakhali ake anawomboledwa ndi anthu a m'mudzi.

Kuchokera tsiku limenelo, Kalabushe sanayankhulenso kwambiri ndi anthu a chilendo.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kalabushe wobwetuka
Author - Gaspah Juma
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Jesse Breytenbach
Language - Chichewa
Level - First paragraphs