Nkhani ya moto
Deborah Namugosa
Rob Owen

Ndikuuzeni nkhani yanga.

Ndimayamba ngati kambaliwali kakang'ono.

1

Ndimasanduka chimoto cholusa mphepo ikandinyamula.

2

Inu ndi ine, ndife abwenzi okondana.

3

Ndimaphika chakudya chanu.

4

Ndimakuunikirani usiku.

5

Ndili ndi njomba zochuluka.

6

Ndine gawo la banja lanu.

7

Koma samalani, mukandiitanira ku nyumba kwanu.

Sindifuna kundisiya ndekha.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nkhani ya moto
Author - Deborah Namugosa, Beatres Nabune, Alison Tukei, Rose Sabano
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Rob Owen
Language - Chichewa
Level - First sentences