Kulumala sikulephera
Agnes Mabururu
Wiehan de Jager

Awa ndi a Agnes.

Iwo ndi aphunzitsi anga.

1

A Agnes amayendera ndodo.

2

Uyu ndi Metobo.

Ndi DJ wa pa
wailesi amene ndimamukonda.

3

Metobo ali ndi vuto la maso.

4

Awa ndi a Moraa, tinayandikana nawo nyumba.

A Moraa ndi alimi.

5

A Moraa samamva.

Amagwiritsa ntchito manja poyankhula.

6

Uyu ndi Osero.

Ndi katswiri wa mpira wa miyendo ku sukulu kwathu.

7

Osero alibe manja.

Koma amagoletsa zigoli zambiri mu timu yathu.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kulumala sikulephera
Author - Agnes Mabururu
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Wiehan de Jager
Language - Chichewa
Level - First sentences