Nkhuku ndi Bongololo
Winny Asara
Magriet Brink

Nkhuku ndi Bongololo anali pa ubwenzi. Koma amakonda kuchita masewera opikisana.

Tsiku lina, anaganiza zosewera mpira wa miyendo. Amafuna adziwe kuti katswiri ndi ndani.

1

Anapita ku bwalo la mpira wa miyendo. Ndipo anayamba kusewera. Nkhuku inachita changu, koma Bongololo anachita changu koposa.

Nkhuku inamenyera mpira patali, koma Bongololo anamenyera patali kuposa Nkhuku. Nkhuku inayamba kukwiya.

2

Kenako anaganiza zosewera mpira wa mapenate. Bongololo ndi amene anayamba kukhala pagolo. Nkhuku inagoletsa chigoli chimodzi chokha.

Kenako Nkhuku inakhala pagolo.

3

Bongololo anamenya mpira ndi kugoletsa. Bongololo anabwiza njomba ndi kugoletsa. Bongololo anamenya mpira ndi mutu ndi kugoletsanso.

Bongololo anagoletsa zigoli zisanu!

4

Nkhuku inakwiya chifukwa inagonja. Nkhuku siyinavomereze kugonja.

Bongololo anayamba kuseka chifukwa mzakeyo anakwiya.

5

Nkhuku inakwiya kwambiri ndipo inatsekula mlomo wake ndikumeza Bongololo.

6

Pamene Nkhuku imapita kunyumba, inakumana ndi mayi wa Bongololo. Mayiyo anafunsa, "Kodi wamuonako mwana wanga?"

Nkhuku siyinayankhe kanthu. Mayi wa Bongololo anada nkhawa.

7

Kenako mayi wa Bongololo anamva timawu tating'ono tikulira. "Ndithandizeni amayi!"

Mayi wa Bongololo anayang'ana uku ndi uku ndi kumvetsetsa. Timawu timamveka kuchokera mmimba mwa Nkhuku.

8

Mayi wa Bongololo anakuwa, "Gwiritsa ntchito mphamvu zako zapadera mwana wanga!"

Abongololo amatha kununkha kwambiri, ndipo samveka bwino mkamwa. Nkhuku inayamba kumva kudwala.

9

Nkhuku inageya. Kenako inameza malovu ndi kulavula. Kenako inayetsemula ndi kukhosomola kosalekeza.

Bongololo ananyasitsa mkamwa mwa Nkhuku.

10

Nkhuku inakhosomola mpaka inalavula Bongololo amene inameza.

Mayi wa Bongololo ndi mwana wake anakwera mumtengo kukabisala.

11

Kuchokera tsiku limenero, pali chidani pakati pa nkhuku ndi abongololo.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nkhuku ndi Bongololo
Author - Winny Asara
Translation - Ausward Siwinda, Peter Msaka
Illustration - Magriet Brink
Language - Chichewa
Level - First paragraphs