Kodi nindani angawelenge kufika kumi?
Athieno Gertrude
Salim Kasamba

Kale, kale, mukati mutengo, Mfumu Nyalungwe anayamba kuganizila zamsogolo.

Anaganiza nati, "Nayamba kukalamba ndipo siku lina, nizamwalila. Mfumu yanzelu imasanka wotenga udindo pamene ikalibe kukalamba ndiponso pamene mfumuyo ikali naumoyo wabwino."

Koma vuto inali yakuti azasanka bwanji? Mfumu Nyalungwe analikukonda nyama zonse njila imozi.

1

Mfumu Nyalungwe anaganizila njila yosankila. Anatuma matenga ake kuyenda mumadela onse amthengo. Anawauza kuti akauze nyama zonse kuti zikabwele kunyumba yaMfumu.

Anakonza pwando ndipo anali na uthenga womwe anakonzela nyama zonse.

Matenga anapita kumbali zonse zamthengo.

2

Usiku wa pwando, nyama zonse zinafika panyumba yaMfumu. Nyama zinayimba, zinavina ndipo zinamva bwino kwambili.

Mwezi utacoka naonekela pamwamba pamitengo, Mfumu Nyalungwe ananyamuka naimilila pakati pa lubanza. Nyama zonse zinasiya kuyimba nakuvina. Nyama zinamvesela modeka pomwe Mfumu yawo yinayamba kulankula.

3

Amfumu analankula nati, "Ndakala nili kuganiza kuti ntawi yakwana kuti nisanke omwe nizatulila udindo. Koma cifukwa nikukondani monse munjila imozi, siniziba momwe ningasankile wofunikila kunkala mfumu. Pena apa, naganizila kuti mpikisano unisankile."

4

Mfumu Nyalungwe anagwila mkondo. Nalankula nati, "Woyamba mwa imwe amene azaponya mukondo uyu mumwamba nawelenga kufika kumi mkondo usanafike pansi, iye azakala mfumu."

5

Pomwe Mfumu Nyalungwe anasiliza kulankula, nyama zinamva congo caacikulu kucokela kumbuyo kwao. Atapindamuka, anaona Njovu akubwela kusogolo.

6

Njovu anatenga mkondo kusebenzesa citamba cake. Njovu anakanka mutu wace kumbuyo ndipo anaponya mkondo kumwamba.

"Cimozi! Ziwili! Zitatu! Ah!" Njovu analila.

Mkondo unagwa pansi kuwelenga kunango fika pa zinai. Njovu anakalipa. Mfumu Nyalungwe anamuuza nati, "Unali nawo mpata wako." Njovu inaima nayambapo.

7

Atapita njovu, nyama zinayamba kukambisana mokondwa. Zinasokonezekanso na congo cacikulu cinacokela kumbuyo kwao.

Nguluwe anabwela ndimpamvu nanena nati, "Cokani munjila yanga. Cokani munjila mwanga. Ine nizakala mfumu. Nili na minofu zolimba kwambili. Ndine wampamvu kupambana monse. Nifunika kukala mfumu."

8

Nguluwe anawelamila kumbuyo, anagwila mkondo ndi mpamvu, naponya kumwamba. "Cimozi! Ziwili! Zitatu! Zinai! Zisanu! Ah!" anakuwa.

Mkondo unagwa pansi kuwelenga kutangofika pa zinai ndi cimozi. Anakalipa naponya doti mumwamba.

Mfumu Nyalungwe anati, "Nguluwe, nikuponya kamozi cabe ndipo unali nawo mpata wako." Nguluwe anacokapo napita.

9

Kucoka apo, nyama zonse zinayamba kudandaula, kulankula kuti, "Uyu mpikisano niwovuta kwambili. Njovu mkulu kwambili akangiwa. Nguluwe wampamvu kwambili akangiwa. Kulibe angakoze."

Pamene apo, anamva congo cina kucokera kumbuyo kwawo. Pomwe anapindamuka kuyangana kumbuyo, sanakulupilile comwe anaona.

10

Anaona nyani wamkulu alikubwela. Pamene anali kubwela, nyani anali kuyimba nati, "Ningakwanise. Niziba ningakwanise. Ningakwanise."

Nyani anatenga mkondo nabwelela kumbuyo kwambili. Anabweza zanja kumbuya, antamangila kusogola, analumpa mumwamba naponya mkondo mumwamba.

"Cimozi! Ziwili! Zitatu! Zinai! Zisanu! Zisanu ndi cimozi! Zisanu ndi ziwili! Ah!" analila nyani.

11

Mkondo unagwa pansi kuwelenga kuli pa zisanu ndi zitatu. Nyani anakwiya. Anayamba kuzweta-zweta nakudandaula kukamba zosiyana-siyana pali kulephera kwake. Koma Mfumu Nyalungwe anati, "Ayi Nyani, nikuponya kamozi cabe" Nyani anacokapo napita.

12

Nyama zina zinayamba kubwelela kumanyumba. Pomwe zinali kubwelela kumanyumba, zinaona Insa kapita pakati pa nyama zina kuti afike pa lubanza la mpikisano. Potamanga, anati, "Yembekezani. Yembekezani. Siyani niyese. Ningakwanise. Ningakwanise. Siyani niyese."

Kumva izo, nyama zonse zinayamba kuseka.

13

Mfumu Nyalungwe anazunta nalankula mokalipa nati, "Siyani kumuseka Insa. Nindana ananena kuti nyama zing'ono sizingate kucita zinu zakanga nyama zikulu? Ngati Insa afuna kuyesa, azapasidwa mupata womwe wapasidwa kunyama zina zonse. Mupaseni mupata Insa aponye mukondo."

14

Insa anawelamila mfumu wake, anapindamuka natenga mkondo kukamwa. Anabwelela kumbuyo, nasebenzesa mpamvu zonse zamutupi zake poyamba kutamanga. Pomwe anafika pakati pa lubanza, analumpa mumwamba.

Analekeza kupema, kugwila mpepo mumapwapwa, analekelela mkondo, napunda, "Zisanu ndi zisanu ni kumi!"

15

Nyama zonse zinakala cete. Zinatangwanika.

Mfumu Nyalungwe anafotokoza nati, "Inde, Insa. Kupatikiza zisanu na zisanu ni kumi. Kuli njila zambili zofikila pa kumi."

Mpikisano sunapangidwe kupeza nyama ikulu kapena yampamvu kwambili. Mpikisano unali kufuna kupeza nyama ya nzelu kwambili. Ndiye momwe Insa anakala mfumu pambuyo pakufa kwa Nyalungwe.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kodi nindani angawelenge kufika kumi?
Author - Athieno Gertrude, Owino Ogot
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Salim Kasamba
Language - CiNyanja
Level - Read aloud