Kuyembekeza basi
Mecelin Kakoro
Mango Tree

Sam akonzeka kupita kumuzinda m'mawa muno.

"Basi izafika na 9 koloko," amai ake anena ali kumwemweta.

Kukali ma ola awili kuti 9 koloko ikwane.

1

Sam na amai ake afika ku citeshi na 8:45 koloko.

2

Antu ena ambili anabwela kuciteshi ntawi pafupifupi na 9 koloko.

Papita mpindi makumi atatu, antu akali kuyembekeza.

3

Sam wada nkawa. "Kapena basi yaonongeka," aganiza.

"Mwina sitizakwanisa kupita kumuzinda lelo. Mwina sinizagula unifomu yanga yasopano."

4

Pomwe ntawi itakawanira 9.45 koloko, antu ena anabwelela kumanyumba kwao.

Sam anayamba kulila. "Tizapitilizako kuyembekeza," amai ake anati.

5

Mwazizizi, anamva congo.

Basi ili kuza!

6

Basi yafika pa citeshi na 10 koloko.

7

"Lowani! Lowani!" anena oyendesa basi. "Tacedwa kwambili, lelo."

8

Antu alowa mubasi nankala pamipando.

Basi yayambapo pa ntawi ya 10.10 koloko.

9

"Izayambapo ntawi bwanji basi yobwelela mumazulo muno?" amai ake Sam afunsa.

"Basi yobiliwira izayambapo kucoka kumuzinda ndi nthawi ya 2.30 koloko," ayanka oyendesa basi.

10

Sam aganiza, "Tizafika kumuzinda na 11 koloko."

"Tizakala Ntawi yaitali bwanji tikalibe kubwelela na basi?" waganizira Sam.

11

Mafunso pa nthano iyi:

1. Kodi Sam anakonzeka ntawi bwanji m'mawa?
2. Kodi Sam ndi amai ake anayembekeza ntawi yitali bwanji kuti basi ifike?
3. Kodi basi inacedwa na mpindi zingati?
4. Kodi basi itenga mpindi zingati kufika kumuzinda?
5. Kodi ngati basi yacoka kumuzinda pantawi yake, Sam na amai ake azafika ntawi bwanji kumunzi?

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kuyembekeza basi
Author - Mecelin Kakoro
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Mango Tree
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs