Kuwelenga Kabici
Penelope Smith
Magriet Brink

Sabata lonse aMama K anali kukolola kabici. Doobie, Maya na Duksie amatandiza aMama K mudimba pa Ciwelu kuseniseni.

1

Basi yawasiya ana pa geti polowela mudimba. Ana aona mtolo wa maKabici pafupi pa talakita ya aBaba K. "Ha! Taonani kuculuka makabici" analoza Maya. "Payenela pali makabici zikwi zikwi apa!" anaseka Duksie. "Ayi ayi! koma zikwi ziwili!" anasusa Doobie.

2

AMama K anayembekeza pa geti polowela mudimba. "Moni, moni, ndili okondwela kukuonani ana inu. Sopano tiyeni tiyambe kugwila ncito. Muyenela kuwelenga makabici awa ndikuwalongeza mumabokosi. Makabici alowa kumi ndi awili mubokosi. Nili na mabokosi makumi awili. Ana awili alongeze mabokosi asanu ndi awili paoka paoka. Mwana umozi alongeze mabokosi asanu ndi imozi.

3

Ana anaimilila pamtolo wa kabici. Anakambilana njila zosiyana siyana zowelengela kabici. "Nizawelenga iwili iwili yanga kabici," anati Maya. "Ine nikonda kuwelenga zinayi zinayi," anati Duksie, "chisilizika msanga." "Ine nizawelenga yatatu yatatu kuti nisinthe kawelengedwe!" anati Doobie.

4

Mwamsanga-msanga ana anazaza mabokosi makumi awili. "Mwagwila ncito" anatokoza aMama K. "Taonani makabici ena asalila. Nkumba zanga zikonda kabici. Anati, "Gawilani nkumba kabici yasala." Amama K anafunsa nati, "Mwalongeza ingati kabichi mumabokosi? Kwasala ingati kabici?"

5

Ncito yosatila niyolemba mtengo pamabokosi ndi kutandiza aBaba K kulongeza ma bokosi mu talakita. Ana afunika kulongeza mabokosi kumi kumbali imozi ndiponso mabokosi kumi kumbali ina yatalakita kuti mabokosi ankazikike bwino mutalakita.

6

"Tilipafupi kusiliza!" anati aBaba K. "Tiyeni tione mabokosi amene tifunika kuika kumbali iyi kuti mabokosi ankazikike bwino mutalakita."

7

Mabokosi onse makumi awili awalongeza mutalakita. ABaba K aliza talakita ndipo apita kumsika. "Ngati ningakwanise kugulisa mabokosi onse, ningapeze ndalama zokwanila kuti nikonze kola ya nkumba ndiponso ningagulile ana cowakondwelesa!" anaganiza aBaba K.

8

Kumunda, aMama K na ana atilila zomela na kupyela matepo. Kufika muzuba, bonse balema. Amama K anena kuti, "Nintawi yakuti nikupaseni camene nakukonzelani. Nindani angalotele chamene nakukonzelani lelo?"

9

AMama K apita kukatenga cameneakonza. Ana ayembekezela kuti abwele, ndipo apitiliza kunena muloto comwe aMama K azabwelesa. AMama K abwela ndipo tumba la covala cawo ndilozaza.

10

"Kodi mwalotela zoonadi? Kodi nakukonzelani cani lelo?" AMama K avungulula covala ndipo ma appo agwa pa tebulo. "Taonani ninalotela zoonadi" anati Duksie. AMama K auza ana kuti, "Mukumbukile kugabana mwacilungamo! Kusapezeke otenga kupitilila mwina kuchepekela ena.

11

Paciyambi ana apenda ma appo awili awili. Apenda motele: 2, 4, 6, 8, 10, 12, 14, 16, koma appo imozi yasalila. Pamozi ali khumi asanu ndi awili ma appo.

12

Cosatila, ana agabana ma appo molinganiza. Kwasala awili ma appo. Ana aika ma appo muvyola vao kuti anyamule kunyumba. Kodi mwana aliyense atenga angati ma apple.

13

"Tiyeni tijube ma apple awili kuti tigawane," wanena Duksie. "Kodi aliyense azatenga angati magawo?" afunsa Maya. "Ine niziwa!" amwetulila Doobie.

14

Pamenepa aBaba K afika kucoka ku msika. Talakita ilibe kalikonse aBaba K amwetulila. "Nagulisa yonse Kabici. Sopano ningakonze khola ya nkumba ndipo ningagule bola yanu." "Eh!" asekelela bana.

15

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kuwelenga Kabici
Author - Penelope Smith
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Magriet Brink
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs