Byantaka na Poto Yakufa
Peter Kisakye
Emily Berg

Kalekale, kunali mwamuna zina lake Byantaka. Masiku onse Byantaka anadyesela ng'ombe yake. Byantaka anapasa ng'ombe yake mazi akumwa, koma anali cabe nakapoto kang'ono kamazi.

1

Anapita kunyumba yamzace kuti abweleke poto ikulu. Mzace anavomela kupasa Byantaka poto yake ikulu kwambili. Iye anati, "Vuto yamzanga ni vuto yanga."

2

Patapita masiku ang'ono, Byantaka anapita kugula kapoto kang'ono. Anapita nako kunyumba kapoto. Anaika kapoto kang'ono mu poto ikulu imene anabweleka.

3

Anatwika poto ikulu yomwe inali nakapoto kang'ono pamutu. Anapita nayo poto kwa mzace amene anamubweleka poto.

4

Byantaka anauza mzace nati, "Nabwelesa poto yako. Yabala poto inzake." Mzace anadabwa kuti poto yake yabala poto inzake. Anamuthokoza Byantaka nanena kuti, "Nyumba yako niyodalisika."

5

Patapita masiku, Byantaka anabwelelanso kukabweleka poto kwa mzace. Byantaka analibe cilingo ca bwino.

6

Mwine wapoto mosangalala anayembekezela kuti Bwantaka abweze poto. Mosatila, anayenda kunyumba ya Byantaka ndipo anati, "Nabwela kuzatenga poto yanga."

7

Byantaka anauza mzace nati, "Mzanga, poto yaku inamwalila. Ninalikufuna kuyambapo kuti nibwele kunyumba kwako nikuuze nkhani yacisoni imeneyi."

8

Mzace anaomba mumanja modabwa. Anayamba kukwiya pamaso pake. Anakuwa nauza Byantaka nati, "Nikalibe kumvapo kuti poto yamwalila!"

9

Byantaka anyanka nati, "Mzanga, ufunika kuvomela zinthu izi. Chinthu ciliconse camene cibala cifunika kufa. Nanenso ninasausidwa na imfa ya poto ikulu ija."

10

Mzace anakwiya kwambili ndipo anapita kukadandaula ku mphala. Amfumu anamvesela madandaulo kucoka kwa onse awili. Anapeza kuti mwine wapoto anali olakwa ndipo anaweluza kuti Byantaka angasunge poto yakufa.

11

"Pamene Byantaka anakuuza kuti poto inabala unavomela. Akanena kuti zonse zomwe zibala zifunika kufa, anena coonadi." Amfumu anaweluza mulandu motere.

12

Mzace wa Byantaka anapita kunyumba ngati nkhono. Byantaka anatenga poto kamba kakuchenjela kwake.

13
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Byantaka na Poto Yakufa
Author - Peter Kisakye
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Emily Berg
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs