Galu na Ng'wena
Candiru Enzikuru Mary
Rob Owen

Siku lina kumumana, Galu anapeza mazila mumchenga. Galu anazifunsa nati, "Kodi nindani amene asiya mazila awa apa?"

1

Anapenda mazila kumi ndipo anaganiza kuti yangakale ya Baka. Galu anaika mazila mucola.

2

Anayenda nayo kunyumba mazila nayaika pamalo potuma.

3

Pamene Galu anabwelela kumumana anapeza Ng'wena. Ng'wena anati, "Kodi waonako mazila anga?" "Palibe comwe niziwa pa nkani ya mazila ako," anati Galu.

4

Ng'wena anayamba kufunsa nyama zonse kusakila mazila ake.

5

Ntawi imeneyo, mazila anayamba kukonkomoka.

6

Galu anayesesa kuti asunge ana aNg'wena koma analibe cakudya cokwanila. Ana aNg'wena anali ndi njala ntawi zonse.

7

Siku lina Ng'wena anayenda kunyumba ya Galu kusakila mazila ake. Ng'wena ali imilile panja, anamva kulila njala kwa ana ang'wena.

8

Ng'wena anatamangila munyumba. Ng'wena anakwapula Galu na mucila wace. Galu analila natawila panja.

9

Ng'wena anatamangisa Galu mpaka ku mumana.

10

"Nikululukile, sininaziwe kuti anali mazila ako!" Analila Galu.

11

Ngwena anamukululukila Galu ndipo anatenga ana ake kuti akawapunzise kunyaya.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Galu na Ng'wena
Author - Candiru Enzikuru Mary
Translation - Bether Mwale-Moyo, Moffat Moyo
Illustration - Rob Owen
Language - CiNyanja
Level - First sentences