Cona, Galu na zila
Elke and René Leisink
Elke and René Leisink

Uyu ni Cona.

Uyu ni Galu.

1

Cona na Galu alikuyenda mumuzi wao.

2

Ndipo anaona zila.

Zila linali mumauzu leka.

3

Cona na Galu anapita kwa mbalane.

Anafunsa mbalame nati, "Kodi ili ni zila lako?"

4

Mbalame inati, "Ili si zila langa ai. Pitani mukafunse kazizi. Kapena ni zila lake."

5

Cona na Galu anapita kwa kazizi.

Anafunsa nati, "Kodi ili ni zila lako?"

6

Kazizi anati, "Ili si zila langa ai. Pitani mukafunse baka la mumazi."

7

Cona na Galu anapita kwa baka la mumazi. Anafunsa nati, "Kodi ili ni zila lako?"

8

Baka la mumazi linati, "Ili si zila langa ai. Pitani mukafuse mabaka awili ao. Kapena ni lao."

9

Cona na Galu anapita kwa mabaka nawafunsa nati, "Kodi ili ni zila lanu?"

10

Mabaka awili aja anakana kuti silinali zila lao.

Zila lija linapwanyika pwaa!

11

Munali kamwana kabuluzi!

12

Kamwana kabuluzi kanati, "Kodi amai na atate anga ali kuti?"

Cona na Galu anapeleka kamwana kabuluzi kwa amai na atate ake.

13

Sala bwino Cona.

Sala bwino Galu.

Sala bwino mwana wa buluzi.

14

15
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Cona, Galu na zila
Author - Elke and René Leisink
Translation - Lusaka Teachers
Illustration - Elke and René Leisink
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs