Kalabushe musikana wokambisisa
Gaspah Juma
Jesse Breytenbach

Kale kale kunali musikana zina lake Kalabushe. Musikana uyu anali okambisisa. Amai ake anali anamulesa kukamba kamba koma sanali kumvela.

1

Siku lina amai ake ang'ono amene anali kunkala ku sidya lamumunzi mwamene munali kunkala kalabushe anadwala.

2

Amake Kalabushe, ilisiku anali na nchito kwambili. Cifukwa ca ncito, unali usiku pamene anapasa Kalabushe vakudya kuti apeleke kunyumba ya amai ake an'gono amene anali odwala.

3

Munjla, Kalabushe anakumana na Sinson. Sinson anali cimbwi wamene anasinta nankala muntu.

4

Cimbwi anafunsa camene ananyamula Kalabushe. "Nyama, mandanda na mukaka," anayanka Kalabushe. Amake Kalabushe anali anamuuza kuti asauze aliyense vamene ananyamula.

5

Kalabushe anauzanso cimbwi kuti amai ake ang'ono anali odwala ndipo anali kubapelekela vakudya. Cimbwi anamvela mata yayamba kubwela mukamwa pomwe anaganizila nyama inanyamula Kalabushe.

6

Cimbwi mwamusanga-musanga, anatamangila kunyumba ya amai ang'ono a Kalabushe.

7

Cimbwi anamela amai ang'ono a Kalabushe ndipo anaziyambatika bulangete yao.

8

Pamene Kalabushe anafika, munyumba munali zii. Kalabushe anangena munyumba ndipo anaita nati, "Amai muli kuti?"

9

Pamene anaona kuti palibe wamene anayanka, Kalabushe anangena kucipinda kwamene anali kugona amai ake ang'ono. Cinamudabwisa pamene anaona muntu aziyambatisa bulangete ikulu.

10

"Amai nanga nicani lelo matu anu aoneka akulu?" Kalabushe anafunsa. "Kuti nikazikumvesesa bwino," anayanka Sinson mubulangete.

11

Kalabushe anafunsanso, "Amai, nanga nicani lelo menso anu aoneka akulu?" "Kuti nikazikuona bwino," Cimbwi anayanka.

12

Kalabushe anafunsa momalizila, "Amai, nanga nicani kamwa kanu kaoneka kukula lelo?" "Kuti ningakumele bwino." Pamenepo, Cimbwi anajumpa nakumela Kalabushe.

13

Cifukwa Kalabushe anali kukambisisa, anapitiliza kukamba napamene anali mukati mumala mwa Cimbwi. Anafunsa mafunso ambili.

14

Pomaliza, Sinson analema kwambili cifukwa ca mafunso amene anali kufunsa Kalabushe. Sinson anaganizila kumuvulula Kalabushe.

15

Antu a mumunzi anatandiza Kalabushe na amai ake ang'ono. Kucokela apo, Kalabushe analeka kukambisa antu amene saziba bwino bwino.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kalabushe musikana wokambisisa
Author - Gaspah Juma
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Jesse Breytenbach
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs