Anzanga
Zimbili Dlamini
Catherine Groenewald

Zina langa ndine Simo.

1

Ndine okondwela kwambili kunkala na ntawi yokuuzani nkani pali anzanga.

2

Nili na anzanga okwana anayi ndipo mazina awo ni aya: Oyamba ni Zizo, wacibili ni Lele, wacitatau ni Sisa ndipo osilizila ni Ayanda.

3

Monga mwamene muziwila kuti muntu aliyense kulicintu camene akonda kucita. Zizo akonda kwambili kumenya bola.

4

Lele ni munyamata wamene anvela bwino kusamba mumanzi.

5

Sisa eve akonda kwambili masowela a kalambe. Aya masowela kambili yamankalako ntawi ya usiku ngati kuli mwezi.

6

Ayanda akondesesa kuwelenga mabuku.

7

Niziwa mukati mwamutima mwanu mufunsa kuti, "Nanga ine nimasowela bwanji yamene nikonda kwambili?" Mubola, nipezeka. Kungankale nikusamba, niliko. Kalambe, nicaya. Kapena kuwelenga, niwelenga.

8

Ine kulibe kwamene nipezeka kwenenkwene. Cifukwa nikapezeka na Zizo, nimenya bola.

9

Ngati nili na Lele, nisamba pa manzi.

10

Mukaleta Sisa, nili mukalambe.

11

Waitanidwa munzanga, nanga iwe, nimasowela bwanji amene ukonda kwambili?

12

Bwela timenye bola.

13

Bwela tisambe pamanzi.

14

Bwela ticaye kalambe.

15

Bwela tiwelenge pamozi.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Anzanga
Author - Zimbili Dlamini, Hlengiwe Zondi
Translation - Bether Mwale Moyo, Vision Milimo
Illustration - Catherine Groenewald
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs