Sanga la Njoka
Joseph Sanchez Nadimo
Rob Owen

Munzi wa Sinyaire niwozungululidwa na mapili. Njoka zambili zinkala musanga mumapili. Njoka ikulu anali kuiita kuti Unyalego. Iyi njoka inali kuyofya antu amu munzi kwambili.

1

Siku lina Apiyo, Ajoh na Atieno anayenda kusakila nkuni. Ambuya a asikana awa anauza asikana kuti azicenjela nayo njoka ija Unyalego. "Musakatenge cintu cina musanga, mukasakile cabe nkuni," anati ambuya awo. Manje Ajah eka sanakonke lamula la ambuya ake.

2

Asikana anatenga mukaka, ntoci, kandolo na manzi. Anatenga ntambo nacojubila nkuni. Asikana ananyamuka ulendo.

3

Paulendo pawo anali kuceza nakuseka. Mukulu wao Apiyo anabazizilika, "Shii. Tafika mwamene ankala Unyalego."

4

Atieno anaitana anzake nati, "Onani meno ya Unyalego yagolide. Tiyeni tiyatenge." Apiyo anawakumbukisa mau a ambuya awo kuti asikana asakatenge cintu cina ciliconse koma cabe kusakila nkuni.

5

Ajoh anati, "Siniwakulupilila ambuya. Safuna cabe kuti titenge vintu vamene tifuna. Ine nizatenga aya meno yagolide." Anzake anada nkawa. "Ajoh takuuza kuti osatenga," anati anzake. Ajoh sanatayeko nzelu.

6

Pantawi imeneyo, Unyalego anabwela kusakila meno ake. Anakalipa cifukwa sanayapeze meno ake agolide. Njoka ya Unyalego inamvela asikana akamba na kuseka. Njoka inabisama kumbali kwa njila yamene asikana analikufinika kusewenzesa.

7

Asikana anatwika nkuni zao pamutu, koma ntawi ing'ono, anamvela kuti, "Sssssiiii!" Asikana anawopa ndipo anayesa kubisama. Unyalego anabwela okonzekelatu kuluma.

8

Unyalego anafunsa asikana, "Nindani wamene atenga meno anga?" Kulibe anayanka. Njoka inaganizila kuyesa asikana. Wamena alibe mulandu, azaiimba nyimbo kopanda vuto lililonse. Ndipo uyo, azayenda kunyumba nankuni zake. Uyo wamena alakwa azakangiwa kuiimba. Uyo eve azankala cakudya canga ca masiku atatu.

9

Apiyo anaiimba nyimbo bwino bwino. Na Atieno anayiimba nyimbo iyo.

10

Wosilizila anali Ajoh. Iye anafendelela kumbuyo cifukwa anayopa. Anayamba kuimba. Koma maimbidwe yake yanali yoipa. Unyalego anakalipa kwambili, "Nanga nicani camene sulikuiimba ngati anzako?" Njoka inaziwa kuti Ajoh ndiye wamene anatenga meno yagolide.

11

Unyalego anamela Ajoh. Anzake anatamangila kumunzi ndipo anauza antu amumuzi camene cinacitika.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Sanga la Njoka
Author - Joseph Sanchez Nadimo
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Rob Owen
Language - CiNyanja
Level - Longer paragraphs