Munyamata wamene sanali kukondedwa
Phumy Zikode
Wiehan de Jager

Kale kale kunali munyamata woipa nkope, ndipo kulibe wamene anali kumukonda. Ngankale makolo ake sanali kumukonda. Panyumba, anali kunkala cabe eka pamene banja lake inali kutamba TV.

1

Kusukulu anali kunkala eka pamene ana ena anali kusowela.

2

Anali kuyenda eka kumbuyo kwa anyamata ena pamene anali kudyesela ng'ombe. Anyamata sanali kufuna kuyenda naye.

3

Siku lina anaganiza kucoka panyumba, anayenda mpaka anafika musanga lalikulu kwambili. Anacita manta, koma anamvela bwino popeza kuti kunalibe muntu wokamba naye cifukwa antu sanali kumukonda.

4

Pamene anali pafupi-fupi kuti angene musanga lalikulu kwambili, kankalamba, kadoti, koipa nkope kanabwela. Kanamupasa moni ndipo kanamufunsa cifukwa camene anali kungenela musanga. Munyamata anadabwa kumvela muntu amukambisa. Anauza kankalamba kuti kulibe kwamene anali kuyenda. Anali kuyenda yenda cifukwa kulibe wamene anali kumukonda.

5

Kankalamba kanamufunsa munyamata ngati anali kufuna tandizo. Anayanka mwamusanga nati, "Inde." Kankalamba kanamuuza munyamata kuti kakalibe kumutandiza, munyamata anafunikila kukamyanguta kumenso mpaka kankalamba katube.

6

Munyamata anapezeka kuti kunalibe cina camene angacite komabe kukamyanguta kankalamba cifukwa anali kufuna tandizo. Munyamata anakamyanguta kankalamba, anamyanguta mantongo kumenso. Anamyanguta mamina kumpuno, na madoti yamumatu. Ndipo anamyanguta cinso ca kankalamba mpaka kanatuba kutubilatu.

7

Kankalamba kanamuonga munyamata uyu. Kanati, "Uzapeza vintu vabwino, musanga umu, koma osatenga cintu cili conse. Ubwelese cabe muzhyu wamene uzapeza."

8

Anatamanga munyamata uja ndipo analanganisisa kuti aone vintu vosiyana siyana musanga. Akalibe kungena musanga, kankalamba kanamuitana kuti abwelele. Kankalamba kanati, "Munyamata! Bwelele kuno!" Anatamanga kuyenda kuli kankalamba. Kankalamba kanabwezela kuti, "Usatenge cintu ciliconse pavintu vabwino vonse vamene uzapeza musanga. Ubwelese cabe muzhyu wamene uzapeza." Munyamata anazunguza mutu kuvomeleza ndipo anatamanga kuyenda musanga.

9

Asanangenu musanga, anamva liu likuti "Munyamata! Bwelele kuno!" Munyamata anasokonezeka. Sanaziba camene kankalamba kanali kufuna. Koma anatamanga kuyenda kuli kankalamba. Kankalamba kanati, "Uzapeza vintu vabwino, musanga umu, ubwelese cabe muzhyu wamene uzapeza." Munyamata anazunguza mutu kuvomeleza ndipo anatamanga kuyenda musanga.

10

Pamene anangena musanga, munyamata anamva liu likuti, "Munyamata! Bwelele kuno!" Ndipo munyamata anabwelelanso kuyenda kuli kankalamba. Kankalamba kanati, "Mvesesa vamene nikamba. Ubwelese cabe muzhyu wamene uzapeza. Osatenga cintu cina ciliconse musanga." Munyamata anakalipa cifukwa cakumubweza bweza. Ndipo anatamanga kuyenda musanga.

11

Mukati mwasanga, anapeza mbale yozula ndalama. Anatenga ndalama ndipo anayika mu tumba lake. Pamene apo anakumbukila vamena kankalamba kanakamba. Anatenga ndalama ndipo anabweza mu mbale.

12

Anapitiliza kuyenda. Nipo anaona vovala vokongola vanyowane. Anavula vovala vake ndipo anavala vovala vanyowane. Pamenepo anakumbukila vamena kanakamba kankalamba. Anavula vovala vanyowane ndipo anavala vovala vake vakudala.

13

Anaona muzhyu, muzhyu uja unali woyuma-yuma cifukwa ca zuwa. Munyamata uyu anazifunsa camene kankalamba kanali kufuna kucita na muzhyu uyu. Pafupi na muzhyu panali mbale yacakudya. Cakudya ici cinanunkila bwino kwambili. Cifukwa munyamata anali na njala, anakangiwa kuzilesa, anatenga ndipo anadya cakudya cija.

14

Pamene anasiliza kudya, anaganizila vamene kanamuuza kankalamba, kuti akatenge muzhyu cabe. Anasakila muzhyu koma sanaupeze, unaleka kuoneka.

15

Munyamata anacoka musanga okumudwa. Anayenda kuuza kankalamba vamene vinacitika koma kankalamba sanakapeze.

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Munyamata wamene sanali kukondedwa
Author - Phumy Zikode
Translation - Bether Mwale Moyo, Vision Milimo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - Read aloud