Siku la mwayi la Hamisi
Adelheid Marie Bwire
Rob Owen

Hamisi anali kufunikila yunifomu yovala ku sikulu. Atate ake ananyamuka na Hamisi kuti akamugulile kumaliketi.

1

Koma akalibe kufika kutali, Hamisi anaona mwana munyamata anavala shati yokongola. Hamisi anaganiza, "Maweh! Kuwama shati ija."

2

"Ningafunisise naine kunkala na shati yabwino monga ija yavala uja munyamata," anapitliza kuganiza.

3

"Onani, bagulisa mashati yokongola," anati Hamisi. "Atate, napapata nigulilenkoni imozi," anakamba Hamisi.

4

"Osasewela, cintu camene cifunika ino ntawi ni yunifomu cabe," anakamba atate ake Hamisi.

5

"Nili nandalama zokwanila cabe kugulila yunifonu yako kwasila," anati atate ake.

6

Mwamwayi, kunasala cenji pamene atate ake analipilila yunifomu ya Hamisi. "Kwasala ndalama yokwanila kugula shati!"

7

Ndipo ali namwayi lelo Hamisi! Kodi azasanka shati iti?

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Siku la mwayi la Hamisi
Author - Adelheid Marie Bwire
Translation - Bether Mwale Moyo, Vision Milimo
Illustration - Rob Owen
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs