Cilema sikulephera kucita zinthu
Agnes Mabururu
Wiehan de Jager

Awa ndi a Agnes.

Iwo ndi aphunzitsi anthu.

1

Iwo amagwiritsa nchito ndodo poyenda.

2

Uyu ndi Malizani.

Iye ndi wanyimbo zanga za pamtima za pawailesi.

3

Malizani ali ndi vuto la maso, sapenya.

4

Awa ndi a Mariya.

Timakhala pafupi nawo kumene timakhala.

A Mariya ndi mlimi.

5

A Mariya ndi a gonthi, samamvera.

6

Uyu ndi Sitefano.

Ameneyu ndiye aposa anyamata ena onse polowetsa zigoli m'masewera a mpira.

7

Sitefano alibe manja, koma agolesa kwambili mu gulu latu la a mpira.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Cilema sikulephera kucita zinthu
Author - Agnes Mabururu
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Wiehan de Jager
Language - CiNyanja
Level - First sentences