Basi ikulu yobilibila
Mecelin Kakoro
Mango Tree

Kunali basi imozi cabe mumunzi wa Ebei.

Inali ikulu ndiponso yobilibila.

Inali ya congo kwambili.

1

Siku lina, amake Ebei anati, "Mailo tizayenda ku tauni tikagule yunifomu yako."

2

Ebei anakondwela kwambili. Ebei na amai ake anali kufunika kukwela basi poyenda.

Usiku uyo, Ebei anakangiwa nakuti agone.

3

Kuseniseni, Ebei anauka ndipo anavala, amai ake akalibe nakubwela kuti amuuse.

4

Ebei na amai ake anayenda namendo ku citesheni ca basi.

Anayembekeza basi ikulu yobilibila Ebei na amai ake. Koma basi siyinafike.

5

Antu ena anafika pa citesheni ca basi. Anadandaula antu cifukwa basi inacedwa kufika.

"Kodi basi yatisiya?" Anafunsa.

6

Ebei anada nkawa. "Sitizakwanisa kuyenda ku tauni. Siniza kwanisa kutenga yunifomu yanga," anaganiza.

7

Antu ena analema kuyembekeza, ndipo anayenda kumanyumba. Koma Ebei analila ndipo anakana kuyenda kunyumba.

Amai ake anamutontoza nati, "Tizayembekezako pang'ono."

8

Mwazizizi antu anamvela congo. Npipo anaona kakungu mu mpepo.

Yabwela basi!

9

Koma basi iyi siyinali yobilibila. Inali yofuwila. Basi iyi inali yofuwila ndipo yaing'ono.

Antu amene anali kuyembekeza anapenya basi. Sanakwele mu basi.

10

"Ngenani! "Ngenani!" anakuwa oyendesa basi. "Tacedwa kwambili lelo." Oyendesa basi anakamba."

11

Ebei na amai ake anayambilila kukwela.

Kosataya ntawi, antu onse anakwela basi yaing'ono yofuwila.

12

Ebei analangana panja pa windo.

Anaona antu ena pa citesheni ca basi.

13

Antu ambili ena anali kutamangila kuti akwele basi. Koma anacedwa.

Basi inazula. Basi yofuwila, inayambapo kuyenda ku tauni.

14

"Kodi basi ikulu yofuwila ilikuti?" anafunsa amake Ebei.

"Yafa," anayanka oyendesa basi. "Tiyikonza. Izabwela mailo," ananena.

15

Ebei sanavutike na kaonekedwa ka basi. Sanavutike na kucepa kapena kukula kwa basi.

Anakondwela cifukwa iyi basi inali kuyenda ku tauni!

16
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Basi ikulu yobilibila
Author - Mecelin Kakoro
Translation - Bether Mwale Moyo
Illustration - Mango Tree
Language - CiNyanja
Level - First paragraphs