

Mandu amakhala ndi agogo ake, azakhali komanso amalume ake. Anali ndi nkhuku ya thadzi, mbuzi, nkhosa komanso nkhumba.
Nkhukuyo inkakhala mu khola laling'ono. Mbuzi, nkhosa ndi nkhumba zinamangiriridwa kuseri kwa khoma. Agogo akewo anali ndi moyo wa thanzi. Azakhali ndi amalume amathandizira ntchito.
Izi zinasintha patatha zaka zochepa. Agogo ake a Mandu anakalamba ndipo sankamva komanso kuona bwinobwino.
Azakhali ake anayamba kudwala ndipo sadathenso kuthandiza ntchito zapakhomo.
Amalume ake ankagona nthawi zonse ndipo sadathandize kudyetsa ziweto.
Ziwetozo zinkachita phokoso kwambiri chifukwa choti zinali ndi njala.
M'nyumba munali mwakuda kwambiri chifukwa azakhaliwo sanakonzemo.
Mandu anali wotopa nthawi zonse. Tsiku ndi tsiku amapita kukasaka chakudya cha onse pakhomopo.
Mandu sakanatha kupitiriza moyo umenewu. Iye anafunsa agogo ake kuti apeze njira yothanirana ndi mavutowo. Iyeyu anali osasangalala chifukwa agogo akewo sanamumvere.
Azakhali ake odwala aja anati, "Zomwe ndikufuna ndi zoti ndizitha kugona usiku komanso kudzuka m'mawa."
Amalume ake aulesi aja anati, "Gulitsa ziwetozo ndipo ugule chakudya cha agogo ako. Azigona ndipo sakusowetsaso mtendere."
Mandu anakwiya kwambiri. Iye anati, "Amalume, mukudziwa kuti sindingagulitse ziweto. Ndi chuma chokhacho chomwe ndili nacho."
Usiku wina Mandu anadzuka nakhala maso. Anakumbukira za bambo wina wanzeru yemwe anthu amakhulupirira kuti ali ndi njira zothetsera mavuto onse.
Mandu ananyamula ziweto zake ndi kupita nazo kwa bambo wanzeru uja. Anamanga mbuzi, nkhosa ndi nkhumba pa chingwe ndipo nkhuku anainyamula m'manja.
Mandu anafika kunyumba kwa Bambo wanzeru uja atatopa komanso ali ndi njala.
Atafotokoza vuto lake, bambowo anati, "Ndikuthandiza koma uyenera uchite zomwe ndinene."
Mandu anayankha, "Ndichita chilichonse kuti ndithetse vuto langa."
Bambo wanzeru uja anati, "Siya ziweto zako kuno ndipo bwerera kunyumba kwako."
Mandu anati, "Koma ziweto zanga ndakhala nazo kwa nthawi yaitali. Ndi chuma chokhacho chomwe ndili nacho."
Bambo wanzeru uja anati, "Ndinakuuza kuti nditha kukuthandiza koma uchite zomwe ndinene."
Mandu anali kufuna thandizo pa vuto lake. Anasiya ziweto zake ndipo anabwerera kwawo.
M'nyumba mwake munali ziii kwambiri komanso mopanda kanthu. Aliyense anazisowa ziweto zija. Agogo ake a Mandu amadandaula chifukwa analibe mkaka wochokera ku mbuzi ija.
Amalume ake anati, "Ndife osauka kwambiri, aliyense akutiseka."
Mandu sakanatha kupitiriza kuthana ndi madandaulowo. Kupatula apo, nayenso anali atazisowa ziweto zake.
Iye anabwerera kwa bambo wanzeru uja kukawafunsa kuti amuunikire. "Moyo ndi wosinthika kwambiri popanda ziweto zanga. Abale anga nawo azisowa kwambiri."
Bambo wanzeru anati, "Ndikuthandiza koma uyenera uchite zomwe ndinene. Pita kwanu ndipo ukawathamangitse agogo ako m'nyumba."
Mandu anati, "Ndichita bwanji zimenezo? Iwo ndi agogo anga ndipo amadalira ine."
Pamapeto pake, Mandu anapita kwawo ndipo anachitadi monga momwe anauzidwira. Iye analibe mtendere wamumtima uliwonse.
Agogo ake analibe kolowera. Iwo amangodziyendera, kuyesetsa kuti asaombane ndi zinthu. Amaombedwa ndi dzuwa masana ndiponso amamva kuzizira madzulo.
Azakhali ake odwala aja analira, "Usandithamangitse!"
Amalume ake aulesi aja analira, "Inenso usandithamangitse!"
Mandu analephera kupitiriza kuchita zimenezi. Anabwereranso kwa bambo wanzeru uja ali wobalalika komanso wokwiya.
Analira nati, "Izi ndachepa nazo. Ndipatseni njira yabwino yothanirana ndi mavutowa"
Bambo wanzeru uja anati, "Eko, tenga ziweto zako pita nazo kwanu ndipo ukawabwenzeretse agogo ako m'nyumba."
Mandu anachitadi monga momwe anauzidwira. Azakhali ake anati, "Ndikonza m'nyumba."
Amalume ake analeka kukhala aulesi ndipo anamuthandiza ntchito Mandu. Onse anakhala osangalalanso.

