Tom anyamula mbale ya nthochi zakupsa.
Tom akupita ku msika kukagulitsa nthochi.
Anthu kumsikako akugula zipatso.
Koma palibe ndi m'modzi yemwe akugula nthochi za Tom. Amakonda kugula zipatso kwa akazi.
"M'dera mwathu, amayi okha ndi omwe amagulitsa zipatso," anthu amatero. "Ndi mwamuna wa mtundu wanji uyu?" anthu amafunsa.
Koma Tom sakugonja. Amaitanira, "Ndiguleni nthochi! Ndiguleni nthochi zokoma ndiponso zokupsa!"
Amayi amodzi anyamula phava la nthochi kuchokera mu basiketi muja. Ayang'ana nthochi zija mosamala.
Amayi aja agula nthochi zija.
Anthu ambiri akubwera pa pamalo a Tom. Iwo akugula nthochi za Tom ndipo akuzidya
Posakhalitsa, m'basiketi muja mulibe kalikonse. Tom akuwerenga ndalama zimene wapeza.
Kenako Tom agula sopo, shuga ndi buledi. Aika zinthuzo mu basiketi yake.
Tom adendekera basiketi pamutu pake ndipo apita kwawo.