

Mphaka ndi Galu amagwirizana kwambiri.
Iwowa anapangana kuti amuyendere nzawo, Mwanapiye pa tsiku lokondwerera kubadwa kwake.
Mwanapiye anali kukhala m'mudzi wina wosiyana ndi anzakewo. Zinkawatengera masiku awiri kuti Mphaka ndi Galu akafikeko.
Mphaka ndi Galu anali ndi makhalidwe osiyana kwambiri.
Galu amakonda kudya komanso kugona ndipo nthawi zina anali wosokoneza.
Mphaka anali wamtima wabwino, wopatsa komanso wodalirika.
Anakumana kunyumba kwa Galu kuti akonze ulendo wawo.
"Ndibweretsa chakudya cha tsiku loyamba," Galu anadzipereka.
"Ndibweretsa chakudya cha tsiku lachiwiri," anatero Mphaka.
Analemba chilichonse ndi cholinga choti asayiwale.
"Zikhala zosangalatsa kumuona Mwanapiye posachedwapa. Papita nthawi chimuonereni nzathu uja," Galu anatero pamene amamuperekeza Mphaka kwawo.
"Zikomo pondiperekeza kwathu," Mphaka anatero kwa Galu.
Anakumana mmawa kwambiri tsiku lotsatiralo kuti ayambe ulendo wawo.
Ankayimba ndi kuvina mosangalala munjira.
Patadutsa kanthawi, anapuma pansi pa mtengo waukulu. "Ndili ndi njala! Tiye tidye," adatero Mphaka.
Galu anagawa zakudya mu mbale ziwiri mofulumira. Chakudyacho chinali chamafuta ochuluka komanso chamadzimadzi.
Mphaka anafunsa, "Izi ndi zakudya zimene wabweretsa za awirife?"
Mphaka anakwiya chifukwa nzakeyo sanabweretse chakudya chimene anagwirizana kuti abweretse. Sanadye zakudya za Galuzo.
"Ndi chifukwa chiyani ukudikira?" Galu adafunsa. Iye ankayembekezera kuti Mphaka aleka kudandaula ndipo adya.
Monyansidwa, Mphaka adafunsa, "Ndi chifukwa chiyani wabweretsa chakudya chomwe umakonda iwe wekha?"
Galu ankadya mwaphuma kwambiri mpaka mbale yake inagudubuka.
Zakudya zake zonse zidatayikira pansi.
"Usadandaule nzanga," Mphaka adatero.
Mphaka adatulutsa buledi owoneka bwino. Anayamba kudya.
Galu anayang'ana chakudya cha Mphaka ndi maso opempha.
Pamene Mphaka anatsiriza kudya, analongeza ndi kumuuza Galu, "Tingathe kupitiriza ulendo wathu?"
Sanayankhulitsane popitiriza ulendo wotsalawo. M'mimba mwa Galu munalira chifukwa cha njala.
Madzulo wake, Mphaka anadzigawira chakudya chake. Anagona ali wosangalala kuti anali atabweretsa chakudya chokwanira.
Galu anagona ndi njala.
M'mawa, Mphaka anadya kadzutsa wochepa. Galu sankaleka kuyang'ana chakudya cha Mphakacho.
Mphaka anagawirako Galu chakudya china.
Galu anati, "Undikhululukire, ndinali wodzikonda kwambiri."
Mphaka anayankha, "Tiye tidye limodzi."
Onse anakhala nkumadya.
Pamene anali kupitirira ndi ulendo wawo, anakhalanso abwenzi!
Anafika ku nyumba ya Mwanapiye mu nthawi yake.
"Ulendo wanu unali bwanji anzanga?" Mwanapiye anafunsa.
Uku akusekererana, Mphaka ndi Galu anayankha, "Unali bwino kwambiri."
Lidali phwando lokondwerera kubadwa lopambana.
Anadya, anaimba komanso anavina!


