Atsogoleri Ang'ono: Kukhala ndi malo aukhondo
Ruth Asuquo

Dera la Lumbazi likanakhala dera labwino, koma derali linali losasamalika.

Mabotolo osweka anali pena paliponse. Zipepala zinali ponseponse ndipo mpweya wake unali wonunkha kwambiri.

1

Ana ankavulala ndi mabotolo oswekawo.

2

Kukakhala mphepo, zipepala zinkaulukira m'mitengo komanso pa madenga.

Izi zinachititsa kuti anthu ambiri asamapite ku Lumbazi.

3

Tsiku lina, mnyamata wa zaka 9, Chike, anauza anzake maganizo omwe anali nawo.

"Tiyeni tikonze limodzi dera lathu. Titha kusesa, kutola mabotolo osweka komanso kukonza motayiramo zinyalala kunyumba zathu komanso m'misewu yathu."

4

"Izi zitithandiza kuti tikhale aukhondo. Zikopa anthu amadera ena kuti abwere kudzaona dera lathuli," anapitiriza Chike.

5

Akuyankhula choncho, Obi anati, "Nditola mosamala mabotolo oswekawo. Ndiwaika pamalo pamene sangathe kutivulaza."

6

Felix anati, "Ndibweretsa imodzi mwa ndowa zakale (zokutha) zomwe zili m'nyumba yakwathu kuti tigwiritse ntchito ngati chotayiramo zinyalala."

7

Anagwirira ntchito limodzi tsiku lililonse.

Kuyambira tsiku limenelo, dera la Lumbazi linakhala dera la umoyo wabwino komanso lotetezeka kwa aliyense wokhalamo.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Atsogoleri Ang'ono: Kukhala ndi malo aukhondo
Author - Ruth Asuquo, Gideon Eyo
Translation - Peter Msaka
Illustration -
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs