Fulu ndi dolo
Ntombifuthi Ncwayiba

Kale kale, nyama za mtchire zinasowa madzi.

Zinayang'ana kulikonse koma osapeza kanthu.

1

Zinachita msonkhano kuti zipeze njira yothetsera vutolo. Nyama zonse zinabwera kumsonkhano kupatula Nkhandwe.

Nkhandwe inati, "Ndingabwere bwanji ku msonkhano koti kuli fulu onunkha?"

2

Pa msonkhanopo, nyama zinagwirizana zokumba chitsime.

Gwape anati, "Chitsime chathu chikhala chachikulu ndi chakuya. Chikadzadza, sitidzasowaso madzi."

3

Nyamazo zinayimba ndi kuvina zikulandirana kukumba chitsime.

Pamapeto, madzi anatuluka ndipo chitsime chinadzadza.

Nyama zinakondwa koposa. Zinali zisanawalawe madzi okoma chotere.

4

Tsiku lina, nyama zinazindikira kuti winawake akumasamba komanso kuwadetsa madziwo.

Nyamazo zinayamba kulondera chitsime chija.

5

Kalulu tsiku limenero amalondera. Nkhandwe inabwera ndi chingwe chake chochitira masewera ojowa.

"Ukutani kuno?" Nkhandwe inafusa.

"Ndikulondera madzi athu," Kalulu anayankha.

6

Nkhandwe inafusa Kalulu kuti azisewera.

Masewera ake ndiomangana ndi chingwe, kutseka maso ndi kuwerenga mpaka sauzande.

Kalulu anavomera kusewera.

7

Nkhandwe inamumanga Kalulu, amene anatseka maso ndi kuyamba kuwerenga.

Nkhandwe inamwa madzi ndi kusambiramo.

Pamapeto, Nkhandwe anatengako madzi ndi kuchoka. Kalulu akuwerengabe.

8

Kalulu anamaliza kuwerenga ndi kutsekula maso ake.

Nkhandwe inali itapita.

Kalulu anakuwa kuitana nyama zina kuti zidzamumasule.

9

Nyama zinapitiliza kulondera chitsime chija, koma onse analephera kuigwira nkhandwe.

Fulu anati, "Ndisiyeni ndilondere ine." Anajowera muchitsime kudikira Nkhandwe.

10

Nkhandwe itafika, inalingalira, "Kulibe aliyese kuno!" inayamba kumwa.

Kenako inamva china chake kuluma lilime lake. Kenako, inakokeledwa pasi pa madzi!

Nyama zinazo zinabwera zikuthamanga zitamva Nkhandwe ikulira ndi kukhavira m'madzi.

11

Nyama zinaimanga Nkhandwe ija.

Fulu anati kwa Nkhandwe, "Unalakwira tonse ife. Ulangidwa." Nyama zinamuyamikira Fulu ngati dolo wawo.

Kuchokera tsiku limenelo, nyamazo zinakondwera kumwa madzi oyera popanda vuto.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Fulu ndi dolo
Author - Ntombifuthi Ncwayiba
Translation - Peter Msaka
Illustration -
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs