

M'mudzi wa Misoya, munali mtsikana wina ochenjera, dzina lake Nomusa. Amakhala ndi agogo ake amene amalima chimanga.
Anthu ambiri m'mudzimu samatha kuwerenga ndikulemba. Amadalira ulimi.
Nomusa amakonda kupita kusukulu, ndipo agogo ake amamunyadira.
Tsiku lililonse akachoka kusukulu, agogo ake amamupatsa ntchito za kumunda.
Amayenera kuthamangitsa apusi ndi mbalame zimene zimadya mbewu.
Nomusa zimamuvuta kuti athamangitse apusi ndi mbalame masana onse. Kotero nthawi imamuchepera kuti amalize ntchito ya kusukulu.
Ana ambiri m'mudziwu amajomba kusukulu chifukwa amagwira ntchito za kumunda.
Tsiku ndi tsiku, Nomusa amatopa kwambiri ndi zothamangitsa mbalame ndi apusi.
"Ndapeza njira ya bwino," analingalira.
Nomusa anamangirira timitengo tatitali tiwiri pamodzi. Anavalika timitengoto zovala zake zogwirira ntchito.
Anaimitsa mitengoyo ndikuvalika chipewa chake.
Chinasanduka choopsezera!
Nomusa anaika choopsezeracho pakati pa munda wa chimanga.
"Choopsezerachi chizindigwirira ntchito pamene ine ndikulemba za kusukulu. Agogo aziganiza kuti ndili m'munda," Nomusa anamwetulira payekhayekha.
Tsiku ndi tsiku, amatenga chikwama chake cha kusukulu kupita kumunda.
Amavala yunifolomu yake ndi kuvalika choopsezera zovala zogwirira ntchito.
Kenako, amalemba ntchito yake ya kusukulu ali pansi pa mtengo.
Masiku anapitapo ndipo Nomusa anaganiza,
"Agogo sadzadziwa za nzeru yanga yakuyayi."
Nomusa anasangalala komanso kuzizwa pakamodzi.
Apusi ndi mbalame sizimafika m'munda muja.
Masana a tsiku lina, agogo a Nomusa anapita kumunda kukathyola dowe.
Kumunda kunali ziii. Kunalibe apusi ndi mbalame.
Agogo analingalira, "Nomusa akugwira ntchito yake bwino."
Agogo anaitana, "Nomusa! Nomusa! Uli kuti?"
Kunalibe yankho.
Kenako, anaona choopsezera mbalame chija pakati pa munda, chitavala zovala za Nomusa!
Agogo atazindikira zimene Nomusa anachita, anakondwera naye.
Anaganiza, "Apa unaganiza mwanzeru. Nomusa sakuyeneranso kumapita kumunda kukathamangitsa apusi ndi mbalame."
Aliyense m'mudzi muja anakonda nzeru za Nomusa. Onse anayamba kugwiritsa ntchito zoopsezera m'minda yawo.
Zoopsezerazo zimathamangitsa apusi ndi mbalame.
Ana amapita kusukulu m'malo mokathamangitsa apusi ndi mbalame.


