Ng'oma ya Magezi
Hlekane Paulinah Baloyi

Magezi ayamba kuimba ng'oma yake ya makaka akuda ndi oyera.

1

Ana amuzungulira.

Akuimba motsatira ng'oma.

2

Akuimba, "Kodi Masingita wakwatiwa ndi yani?
Wakwatiwa ndi m'modzi wa ife."

3

Amayi akuvina mozungulira kutsatira kulira kwa ng'oma.

4

Abambo akuvina motsitsa ndi kukweza matupi awo.

5

Mudungwazi atembenuza maso ake awonetsa mavinidwe ake oseketsa.

6

Abambo akuyimba miluzu ndi kugwedeza mitu yawo motsatira ng'oma.

7

Amayi akugwedeza ziuno zawo ndi kululuta.

Aliyese akusangalala.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Ng'oma ya Magezi
Author - Hlekane Paulinah Baloyi
Translation - Peter Msaka
Illustration -
Language - ChiChewa
Level - First words