Mama Sofi, olimba mtima
Thandiwe Dlodlo
Simon Mokoena

Masana a tsiku lina, Khosi amangozungulira, kusowa zochita.

Amayi ake anapita kumunda, anamusiya Khosi yekha.

"Nde ndizitani?" Khosi anadzifunsa.

1

Ganizo linafika m'mutu mwa Khosi.

"Ndikasambire ku mtsinje, koma ndipita ndi ndani?" Khosi anaganiza.

Nthawi imeneyo, Mama Sofi amadutsa kupita ku mtsinje. Ananyamula basiketi yodzadza ndi zovala.

2

"Nditsatira Mama Sofi kumtsinje!" anatero Khosi mu mtima mwake.

"Kodi ndingapite nanu kumtsinje?" anafunsa Khosi. Mama Sofi adamwetulira ndikugwedeza mutu.

Ali mnjira Nozipho naye adawalondola. Nozipho samakonda kusambira koma ankasangalala kuona ena akusambira.

3

Kumtsinje kuja Khosi anati, "Lero, ndasiya kusambira kumadzi ochepa, ngati mwana! Ndiwaonetsa anthu kuti ndithanso kusambira kwakuya."

Anajowera m'madzi. Phavaaa!

Nozipho amangoyang'ana kuchokera patali.

4

Nozipho akuonerera, ana onse amasangalala kusambira mumtsinje.

Amasambira mwaphokoso.

Amakuwirana mosangalala.

5

Nozipho anaonetsetsa, chinachake sichinali bwino. Khosi amasambira kutali ndi anzake. Nozipho anayandikira ndi kuonetsetsa.

Anachita mantha ndi zimene anaona, anathamangira kwa amayi amene amachapa.

"Ndithandizeni! Khosi akumira," anakuwa Nozipho

6

Mwachangu, Mama Sofi anajowera m'madzi. Anapita pansi pa madzi.

Anapita pansi ndikutuluka, kulowanso ndi kutuluka, kusakasaka Khosi.

Anamugwira Khosi pa dzanja ndikupita naye malo osaya kwambiri. Kenako, Mama Sofi anamunyamulira Khosi kumtunda.

7

Mama Sofi anadutsa pamene panali ana ndi amayi ena amene amalira ndi kukuwa.

Nozipho anatsatira pambuyo. Mama Sofi anamubereka Khosi kupita naye ku chipatala cha m'mudzimo.

8

Kuchipatala, Mama Sofi anapeza a nesi Nozolo amene anathamanga kudzathandiza.

Anesi anamutenga Khosi mwachangu kupita naye muchipinda, manesi ena anathamangirako kukathandiza.

"Ali bwino! Mwamwayi sanakhalitse m'madzimo!" anatero a nesi Nozolo.

9

Mama Sofi mtima unakhala m'malo.

Aliyense pachipatalapo anawayamikira Mama Sofi chifukwa cholimba mtima komanso luso losambira.

"Ndine okondwa kuti ndateteza moyo," anatero Mama Sofi modzichepetsa.

10

Nkhani inafika kwa mfumu ya m'mudzimo. Anatumiza mthenga kuti akawayitane Mama Sofi.

Mama Sofi adawafotokozera amfumuwo momwe anaphunzirira kusambira.

"Ndili mwana, mnzanga ankakhala kutsidya lina la mtsinje, ndipo madzi anali mbali ya moyo wathu wa tsiku ndi tsiku," adatero.

11

Amfumu anaitanitsa msonkhano ndi kulengeza kuti apereka mphoto kwa Mama Sofi kamba kolimba mtima.

Amayi analuluta, abambo anaimba malikhweru, ana anakuwa ndi chisangalalo. Kuchokera tsiku limenero, ana amakonda kulondora Mama Sofi, kumaimba, "Palibe chingandigwire ine, ndili ndi Mama Sofi, olimba mtima!"

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Mama Sofi, olimba mtima
Author - Thandiwe Dlodlo
Translation - Peter Msaka
Illustration - Simon Mokoena
Language - ChiChewa
Level - First paragraphs