Kukoma mtima kwa Masozi
Tshedza Tlhako
Busisiwe Ndlovu

Kale kunali mtsikana wina dzina lake Masozi.

Masozi amakhala kumudzi ndi amayi ake komanso agogo ake aakazi.

1

Tsiku lina, amayi ake anamutuma kukapereka uthenga kwa azakhali ake m'mudzi wina.

"Udzere njira ya nthawi zonse," mayi ake anamukumbutsa Masozi.

2

Masozi anadzera njira ija kupita kwa azakhali ake ndipo anapereka uthengawo.

Ali m'njira kubwerera, anamva mawu ofooka m'mbali mwa msewu, "Ndithandizeni chonde."

3

Masozi anayang'ana uku ndi uku ndipo anawona mayi wina atagona m'mbali mwa msewu.

Anapereka moni ndi kufunsa, "Ndi chifukwa chiyani mwagona pamenepa?"

4

Mayiyo anayankha, "Ndafooka ndikudwala, ndipo kwathu ndi kutali."

Masozi anamva chisoni.

5

Anamuuza mayiyo, "Ndikutengerani kwathu chifukwa ndi pafupi."

Masozi anamuthandizira mayiwo kudzuka. Anayenda pang'onopang'ono mpaka anakafika.

6

Masozi ndi amayi nkomanso agogo ake anawasamala mayiwo mpaka anapeza bwino.

7

Mayiwo anayamikira kwambiri pomusamala.

Anamuthokoza Masozi pokhala mwana wolimba mtima ndi wosamala.

8

Mayiwo anati kwa Masozi ndi banja lonse, "Sindidzaiwala zimene mwandichitira.

Pakapita masiku atatu, ndikufuna munene zimene mumafuna."

9

Patapita masiku atatu, Masozi limodzi ndi amayi ake ndi agogo ake ananena zofuna zawo.

Chofuna choyamba chinali kukhala ndi nyumba yokongola.

10

Chachiwiri chinali kukhala ndi nkhalango pafupi ndi nyumba yawo kuti asamathe mtunda kukatola nkhuni.

Zofuna zawo zonse zinakwaniritsidwa, monga mayi uja ananenera.

11

Masozi ndi banja lake anakhala moyo osangalala mnyumba yawo ya pafupi ndi nkhalango.

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Kukoma mtima kwa Masozi
Author - Tshedza Tlhako
Translation - Peter Msaka
Illustration - Busisiwe Ndlovu
Language - ChiChewa
Level - First sentences