

Takondwa amakonda kusangalala.
Takondwa amayendera njinga.
Abale ake ndi anzake amamukonda kwambiri.
Takondwa amakonda nyimbo.
Anzake amakonda kuvina ndi kumuikira nyimbo.
Anzake a Takondwa anaika sipika yomverera nyimbo pa njingayo .
Akadina batani mbali inayi, nyimbo zimalira.
Takondwa amatha kudziongola ndi kuvina panjinga yake.
Amayesera kuvina payekha, kenako amavina ndi anzake.
Tsiku lina anzake anaona mpikisano ovina utalengezedwa munyuzipepala.
Anawafusa mayi a Takondwa ngati angakalembetse ku mpikisanowo.
Mayi a Takondwa anavomera.
Anzake a Takondwa anabwereka foni ya mayi ake ndi kujambula mavinidwe awo.
Anamujambula Takondwa akuvina nyimbo ya kumtima kwake, kenako anatumiza mavinidwewo kumpikisano.
Takondwa anamusankha kukachita nawo mpikisano!
Tsiku la mpikisano linafika.
Takondwa anavala malaya ake a nyuwani.
Nyimbo zitayamba, anayenda mwadongosolo ndi mokondwa.
Anthu ochemerera anakuwa, "Takondwa! Takondwa!"
Zoona zake, anali dolo ovina tsiku limenelo.
Takondwa anapambana ndipo analandira mphoto zambiri.

