Nyumba yathu ndi nyumba yanu
Vyandeh Terkule
Vyandeh Terkule

Mtema anali munthu wopanda pokhala. Ankasaka zipatso mu nkhalango.

Nthawi zina ankagona konko, anyani ankamuona kuchokera m'mitengo ndi m'zitsamba.

1

Anazungulira m'nkhalangomo ndipo anaona mitengo yambiri.

"Mitengoyi kuno ikungowonongeka," Iye analingalira.

2

Atatopa ndi kuzungulira, anakhala pansi, natsamira umodzi mwa mitengoyo ndi kugona.

Mitengoyo inamamupatsa mthunzi ndipo mbalame zinkauluka uku zikuimba mingoli yokoma.

3

Anayamba kuganiza.

"Nditati ndadula mitengo ingapo, nditha kupanga ndalama ndi kukhala ndi nyumba zapamwamba zambiri."

4

Analowa m'mudzi ndi kukabwereka macheka. Anayamba kudula mitengo.

Nyaniyo anamupempha, "Chonde, musadule mitengoyo. Ndi nyumba zathu komanso nyumba za mbalame. Zipatso zake ndi zakudya zathu."

5

"Ndikufunika ndalama zokonzera nyumba yanga," Mtema anatero.

"Kuononga nyumba za nyama ndi mbalame zambiri kuti mupange malo anu ogona ndi kudzikonda," anatero nyaniyo.

Mtema anamva chisoni, anagwetsa macheka aja, ndikumukumbatira nyaniyo.

6

Mnzakeyo, nyani anapereka maganizo oti atha kugwiritsa ntchito matope kuwumba njerwa ndi kugwiritsa ntchito udzu ndi mitengo kumanga khumbi.

Kutero, ambiri mwa iwo atha kukhala ndi malo okhala.

7

Mtema anavomera. Anayamba kumuyendera nyaniyo kawirikawiri.

Nyaniyo anamulora iye kuthyola zipatso ndi kuthyola mitengo yosafunikira yambiri mmene anafunira.

Anakhala abwenzi.

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Nyumba yathu ndi nyumba yanu
Author - Vyandeh Terkule
Translation - Peter Msaka
Illustration - Vyandeh Terkule
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs