

M'tawuni ina munali mtsikana wokongola dzina lake Ella.
Anali wamtali, wakuda, wa tsitsi lakuda. Anali ndi maso opatsa chikoka.
Ella anali ndi mano oyera bwino ngati ngale. Anali mtsikana wachifundo komanso wolimbikira ndipo samawavutitsa makolo ake.
Chinthu chimodzi chimene chinkawadandaulitsa makolo ake chinali chidwi chake chofuna kudziwa zinthu. Ankafunsa mafunso achilendo kwambiri.
Mwachitsanzo, pensulo yake itathyoka, Ella anawafunsa mayi ake nati, "Amayi, kodi pensulo yanga yapita kumwamba?"
Makolo ake anatopa ndi mafunso ake ochuluka, ndiye nthawi zina, sankamulabadira.
Komabe, mlongo wa wake, Henry, ankamvetsera mafunso ake. Mvula ikugwa, iye anafunsa nati, "Kodi mvulayo ndikulira kwa mitambo?"
Mlongo wakeyo anaseka ndi kuyankha kuti, "Ayi!" Anapitiriza ndi kumufotokozera kuti mvula imagwa pamene nthunzi ya m'mlengalenga yazizira.
Tsiku lina, Iye anaganiza zopita kukayenda. Akuyenda, anawona mtengo wa apozi ndipo mwangozi anathyola nthambi yake.
"Oh, ikufunika adokotala," Ella anatero. Modabwitsa, mtengowo unayankha nati, "Inde, ndikufunika adokotala."
Ella anadabwa ndipo anafunsa nati, "Zatheka bwanji kuti muyankhule." Mtengowo udayankha nati, "Ndine mtengo umene ungathe kuyankha mafunso ako onse."
Ella anawufunsanso nati, "N'chifukwa chiyani mnyamatayu sakukumvani?" Mtengowo unayankha nati, "Chifukwa sanandifunse."
Ella anathamangira kwa mlongo wake ndi kukamuuza zomwe zachitika, awiriwo anathamangira kwa mtengowo. Henry anafunsa nati, "Ndinudi mtengo weniweni?"
Mtengowo unayankha nati, "Ine ndi mtengo weniweni." Awiriwo anavina mokondwa.
Kuyambira tsiku limenelo, iwo sanawavutitsenso makolo awo.
Nthawi zonse akakhala ndi funso amapita kukawufunsa mtengo uja ndipo umayankha mafunso awo.

