Amuna asanu opusa
Chuol Dow Wich
Kenneth Boyowa Okitikpi

Kalekale, kunali amuna asanu opusa omwe ankakhalira limodzi. Iwo ankagawana chilichonse.

Tsiku lina, iwo analibe chakudya. Anaitanitsa msonkhano. "Kodi chakudya tichipeza kuti?" M'modzi wa iwo anafunsa.

1

Panalibe yankho lachangu la funso limeneli chifukwa analibe ndalama komanso anzawo m'deralo.

Ataganiza kwa kanthawi, mmodzi wa iwo anati, "Tiyeni tizipita!" Wachiwiri anafunsa nati, "Kutiko?"

2

Munthu wachitatu anati, "Kukaba chakudya." Wachinayi anati, "Sitikagwidwa?" Wachisanu anati, "Musadandaule ndi zimenezo!"

Amuna asanuwo anapita ku msika kuti akabe chakudya.

3

Atangoyamba kubako, iwo anagwidwa!

Amuna asanuwo anapita nawo kupolisi.

4

Pofufuza, apolisi anafunsa, "Kodi maganizo akubawa anali andani?"

Amunawo anayamba kunong'onezana. Kenako anauza apolisiwo mmene zinachitikira.

5

Munthu woyambayo anati, "Ine ndinangopereka maganizo oti tinyamuke, osati tikabe." Munthu wachiwiriyo anati, "Ndimafuna kudziwa kumene tikupita."

Munthu wachitatu anati, "Tonsefe tinagwirizana kuti tikasake chakudya."

6

Munthu wachinayiyo anati, "Ndinachenjeza kuti tikagwida."

Kenaka munthu wachisanuyo anati, "Tonsefe tikudziwa kuti ndife akuba, n'chifukwa ndinati, 'Musadandaule ndi zimenezo'."

7

Atamva izi, apolisiwo anadziwa kuti amuna asanuwo anatenga nawo mbali pa kubako.

Apolisiwo anamaliza ndi kunena kuti, "Ndi zabwino kugawana chilichonse, kupatula maganizo oipa!"

8
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Amuna asanu opusa
Author - Chuol Dow Wich
Translation - Peter Msaka
Illustration - Kenneth Boyowa Okitikpi
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs