

Madina ndi mwana wamkazi wamkulu wa m'banja la aKarembe.
Banjali limakhala mu mzinda wa Bandiagara.
Madzulo ena, Madina anapita kukatseka chitseko.
Anawona mtsikana ndi mnyamata.
Madina anadabwa kuona ana awiri achilendo.
Iye anawaitana bambo ake, "Bambo! Bambo! Pakhomopa pali ana awiri."
Bambo anathamangira kukhomoko.
Atawaona anawo, bambowo anafunsa nati, "Kodi ndinu ndani? Kwanu ndi kuti?"
Mnyamatayo anati, "Ndine Asama, ndipo uyu ndi mlongo wanga wamng'ono, Yakoromo."
Asama ndi Yakoromo ankaoneka otopa, amantha komanso okhumudwa.
Asama anapitiriza nati, "Tachokera m'mudzi wa Songo, m'dera la Tukombo."
Bambowo anali odabwa kwambiri ndipo anasowa choyankhula.
Madina anati, "Bambo, alowetseni. Atopa komanso ali ndi njala. Akufunika chithandizo chathu."
Yakoromo anayankhula koyamba.
"M'mudzi mwathu munabwera achifwamba. Makolo athu anaphedwa. Chilichonse chomwe tinali nacho chinaonongeka."
Anapitiriza kuyankhula ndi timawu take tachimwana.
"Takhala tikuyenda kwa masiku ambiri. Sitikudziwa kopita komanso chochita."
Kenako, ndi manja otambasula, Bambo anawakumbatira anawo.
"Lowani ana inu, kuno ndi kwanu. Tiyakambirana za izi mukapuma," Iwo anatero.
Anawo anadya mgonero ndi banjalo, chinali chakudya choyamba chotentha patadutsa masiku ambiri.
Kenaka, Madina anatengera Asama ndi Yakoromo ku zipinda zawo.
Kuchokera tsiku limenelo, Asama ndi Yakoromo anatengedwa ngati ana a KAREMBE.
Amasewera ndi kugwira ntchito zapakhomo limodzi ndi ana ena.

