

M'mudzi wina waung'ono kuMalawi, munali sukulu yapamwamba.
Inkatchdewa kuti Chiko, chidule cha dzina loti chikondi.
Sukulu yathu inali malo opereka chiyembekezo ndi chikondi.
Inali sukulu ya ana amasiye monga ine.
Sukulu yathu inazunguliridwa ndi maluwa amitundu yokongola yosiyanasiyana.
Panali ofiira mowala kwambiri, achikasu, ndi amtambo.
Sukulu yathu anali malo osangalalirako.
Ogwira ntchito pa sukuluyi ankatipatsa chakudya ndi mayunifolomu.
Izi zinatichititsa kumva kuti ndife otetezeka komanso okondedwa.
Chipanda sukulu imeneyi, sindikanadziwa kuwerenga ndi kulemba.
Sindikanaphunzira kuwerengetsera manambala kapena kudziwa nkhani zosangalatsa m'mabuku
Aphunzitsi ndi ogwira ntchito pa sukuluyi anali ngati abale athu.
Ankatichititsa kumva kuti ndife ofunikira komanso okondedwa.
Tsiku lililonse ku sukulu tinkaphunzira zinthu zatsopano.
Tinaphunzira ubwino wothandiza ena ndi kukhala othokoza pa zomwe tinali nazo.
Sukulu yanga siinandiphunzitse kuwerenga ndi kulemba kokha komanso inandiphunzitsa kukhala munthu wabwino.
Inandionetsa kuti ndi chikondi, chisoni, ndi maphunziro, titha kuthana ndi chilichonse.

