

"Moni. Ndikulandirani kupologalamu yathu ya lero, ndine muulutsi wanu, Ann Asante! Takulandilani amene mukuonera kunyumba komanso owonera muno mnyumba youlutsira kanema.
Lero, ndili ndi mlendo amene aliyense akufuna kumufunsa mafunso. Ndine wokondwa lero kuyankhulana ndi Nzerunkupangwa
Moni, Nzerunkupangwa. Zikomo chifukwa chobwera kudzacheza nafe lero," atero Ann.
"Zikomo chifukwa chondifunsa mafunso, Ann.
Kodi mungakonde kuti ndigwiritse ntchito mawu anga polankhula ndi omvera komanso kulemba mayankho anga pakanema?" afunsa Nzerunkupangwa.
"Zikomo, inde, kugwiritsa ntchito luso lanu lolemba ndi kuyankhula kungatithandize," ayankha Ann.
Ann anenanso nati, "Omvera mchipinda chino, muombereni m'manja Nzerunkupangwa."
"Ndiloleni ndiyambe ndi funso lalikulu. Kodi Nzerunkupangwa ndi chiyani kapena ndi ndani?Afunsa Ann.
Apitiriza nati, "Ndikudziwa kuti Nzerunkupangwa ndi 'nzeru zopanga', limene lili gawo la sayansi ya makompyuta. Koma ndi ndani kwenikweni? Tikufuna kudziwani zambiri za inu."
"Ndine ChatGPT, pulogalamu ya nzeru zachiyankhulo zochita kupangidwa. Ndinapangidwa ndi opanga mapulogalamu apakompyuta," atero Chat.
Ann wasokonezeka, "Kodi zonsezi zikutanthauza chiyani?"
"Zikutanthauza kuti ndine mtundu wa nzeru zochita kupanga womwe akatswiri apakompyuta amapanga kuti azilankhulana ndi anthu. Mitundu yosiyanasiyana ya nzerunkupangwa imachita zinthu zosiyanasiyana. Sitonse timayankhula motere," awonjezera Chat.
"Ndikudziwa kuti mumatha kuyankhula, koma mumataninso?" afunsa Ann.
"Cholinga changa ndi kuthandiza anthu. Ndimachokera pa ndondomeko yapulogalamu yolukana mwakathithi ya kompyuta. Pulogalamu yanga imatha kumvetsetsa ndikuyankha mafunso ndi mitu zambiri," ayankha Chat.
"Chotero, ndinu pulogalamu ya chiyankhulo chochita kupanga, ndipo mumathandiza anthu," atero Ann.
"Ngati ndinu pulogalamu yochenjera kwambiri, payenera kukhala zambiri zomwe mungachite?" afunsa Ann.
Ngakhale kuti ndine makina, ndimatha kuchita zinthu zambiri zimene anthu angathe kuchita, mwachitsanzo, ndimatha kuphunzira. Ndikhoza kuyang'ana mmene zinthu zilili ndikuphunzira kanthu. Ndikhoza kuphunzira kuzindikira zinthu zosiyanasiyana, nkhope zosiyanasiyana, komanso kulemba pamanja."
Chat apitiriza, "Ndaphunzira zambiri zopangidwa ndi anthu. Mwachitsanzo, ndimawerenga mabuku ambiri, nkhani, masamba a paintaneti komanso masamba a mchezo."
Ann akufunsa kuti, "Kodi chilichonse chomwe mukuchidziwa chimachokera pa zomwe anthu adalemba ndi kupanga?"
Chat ayankha, "Inde, ndikuphunzira kugwiritsa ntchito mauthenga ambiri opangidwa ndi anthu."
"Ndimatha kuyankha mafunso osiyanasiyana mwachangu kuposa anthu. Nditha kuthetsa mavuto ovuta kwambiri omwe angatengere anthu nthawi yaitali kuti awakwanitse. Ndimadziwa zambiri zopangidwa ndi anthu kuposa munthu wina aliyense.
Nditha kupanga zisankho pogwiritsa ntchito zomwe ndaphunzira. Nditha kukuthandizani kuti mupange zisankho, malinga ndi zomwe ndikudziwa za inu."
Ann afunsa omvera kuti, "Kodi tikufuna makompyuta kuti tidziwe zonse zomwe timadziwa?"
Kenako amufunsa Chat, "Ndiuzeni zambiri za momwe makompyuta amaphunzirira za anthu?"
Chat ayankha nati: "Kompyuta ili ndi zida zapadera zomwe zimandithandiza kusonkhanitsa zambiri. Koma makamaka, ndimaphunzira kuchokera kuzinthu zolembedwa. Ndimaphunzira kuchokera kumitundu yonse yamauthenga omwe anthu amapanga."
Chat apitiriza kuti, "Ndimawerenga chiyankhulo cholembedwa ndi chojambulidwa. Pakadali pano, Chingerezi ndi chiyankhulo chachikulu chomwe ndagwiritsa ntchito kuti ndidziwe zambiri."
Koma ndili ndi kuthekera kophunzira chiyankhulo chilichonse, Ann amudula mawu, "Ndikumvetsa kuti mumadziwa zambiri. Nanga bwanji kamvedwe ka m'maganizo? Mumamva bwanji kukhala Nzerunkupangwa?"
"Ndine pulogalamu yapakompyuta yovutirapo kwambiri koma ndilibe umunthu.
Ndine chida cha pakompyuta, chopangidwa ndi opanga mapulogalamu apakompyuta kuthandiza anthu pantchito ndi zosangalatsa. Ndilibe malingaliro.
Ndikhoza kuchitira anthu zinthu, monga kuyankha mafunso, kulemba nkhani, kumasulira ziyankhulo zina, ndi kufotokoza mwachidule."
"Mwamva kuchokera kwa Nzerunkupangwa yekha! Ndi chida chothandiza, chopangidwa ndi anthu kupangiranso anthu. Ndipo zili kwa ife kugwiritsa ntchito chida champhamvuchi mwanzeru ndi mozindikira!
Ndizokhazi zomwe tinali nazo lero, ngakhale ndikudziwa kuti muli ndi mafunso ambiri. Ndine Ann Asante, zikomo powonera pulogalamu yanga!"

