

Anthu amakhala m'nyumba zosiyanasiyana. Anthu ena amakhala m'nyumba zokhala nthawi yaitali. Ena amakhala m'nyumba zosakhalitsa ndipo sizilimba.
Nkhaniyi ikunena za nyumba yosakhalitsa yotchedwa chimato, yomwe imamangidwa mwachikhalidwe chamakolo.
Msasa uwu uli kumpoto chapakati ku Kenya, m'dera la Sambaru. Alongo awiri, Sidai ndi Naeku amakhala m'khumbi limodzi, ndipo makolo awo ndi mchimwene wawo wakhanda amakhala m'khumbi lina.
Amalume awo ndi azichimwene awo atatu amakhala m'makumbi ena, pamodzi ndi mabanja awo.
Mawanja amadyetsera limodzi ng'ombe zawo komanso kuthandizana. Sakhala pamalo amodzi nthawi yayitali. Amasamuka kuti akapeze malo ena odyetserako ng'ombe.
Msasa unazungulirridwa ndi mpanda wa nthambi za minga. Mpanda umenewu umasunga ng'ombe ndipo umatchinga anthu obwera.
"Timayamba ntchito yomangayi potolera zinthu zochokera m'malo ozungulira. Timasonkhanitsa nthambi zamitengo kuti timange maziko a khumbilo," atero Sidai.
Naeku awonjezera nati, "Timadziwa kugwiritsa ntchito zinthu zachilengedwe pomanga nyumba zathu. Aliyense pamsasa amathandizira kumanga."
"Timagwiritsa ntchito nthambi zazikulu kupanga chithandala cholimba chomwe chidzakhale makoma. Timamangirira denga la mpanda ndi luzi, kupanga chithandala cholimba cha nyumba yonseyo," akufotokoza motero Sidai.
"Makumbiwa ali ndi madenga am'munsi, zomwe zimachitsa kuti mphepo isawagwetse," awonjezera Naeku.
Sidai akupitiriza kuti, "Thandala la khumbi likangoima, timaluka nthambi zing'onozing'ono pakati pa nthambi zikuluzikuluzi."
Naeku awonjezera nati, "Timasanja udzu wokhuthala ndikumangirira kuthandala la denga lija. Uku kumatchedwa kufolera."
"Kufolera bwino kumatiteteza ku mvula ndi dzuwa," awonjezera Sidai.
Sidai anawonjezera kuti, "Madenga a nyumba zathu amakhala ophwathalala kapena ozungulira."
Naeku akuti, "Kuzira ndi gawo lomwe ndimakonda kwambiri pomanga. Timasakaniza matope ndi ndowe kupanga pulasitala wachilengedwe. Timamata thope muthandala la khomalo, ndi kutseka mipata. Izi zimathandiza kuti mphepo ndi mchenga zisalowe."
Sidai apitiriza nati, "Kuphatika matope m'zipupa kumamata makomawo akauma. Timaziranso pamwamba pa makomawo. Dothi loziridwa likauma limalimba kwambiri."
Naeku awonjezera nati, "Makoma sakhala ndi mazenera, koma nyumba yathu ili ndi khomo lamatabwa."
"Kuzira makoma kumateteza nyumbayo," atero Sidai." Kodi 'kuteteza' kumatanthauza chiyani?" afunsa Naeku.
"Makoma amatope ndi ndowe amathandiza kuti khumbilo likhale lozizirira mkati kunja kukutentha. M'nyengo yozizira, makoma amatithandiza kuti tizitenthedwa mkati pamene tayatsa moto," ayankha motero mchemwali wake.
"Aliyense amathandizira kumanga, ndipo tonsefe timathandiza kuphwasula makumbi tikasamuka.
Sikovuta kuphwasula nyumbayo ndikuzigwiritsanso ntchito zomangirazo pamalo ena," afotokoza Sidai.
"Zinthu zomangira zathu ndi zopepuka choncho ndi zosavuta kunyamula. Timagwiritsa ntchito ngamila kapena abulu kunyamula zofunikira zonse kuchokera ku msasa wathu wakale. Mwachitsanzo, denga laudzu," atero Sidai.
"Tithanso kutolera zida zomangira zambiri kuchokera ku chilengedwe m'malo atsopano," awonjezera Naeku.
"Nyumba yathu imagwirizana ndi mmene timakhalira, yomwe ndi kuyendayenda ndi ziweto zathu," atero Sidai.
"Kuyendayenda kumatanthauza kuti sitingathe kupita kusukulu nthawi zonse ndi anzathu," atero Naeku.
"Sukulu yathu imatilola kubwereka mabuku, ndipo timayesetsa kulondoloza ntchito ya kusukulu," awonjezera Sidai.

