

Tizilombo timakhala m'nyumba zosiyanasiyana. Tizilombo tina timakhala pamodzi m'magulu akuluakulu, tina timakhala tokha.
Nkhaniyi ikunena za Gang'a ndi Teketeke - chiswe chachikazi chiwiri chomwe chimakhala mtsala lina kumwera kwa dziko la Kenya.
Atsikanawa amakhala m'gulu lina la chiswe pafupifupi 80,000.
Gulu la chiswe limakhala m'chisa chopangidwa ndi dothi. Chisachi chikhoza kukhala pansi pa nthaka, kapena pamwamba pa nthaka, kapena malo onsewo.
Mbali ya chisa imene tingaone pamwamba pa nthaka ndi chulu cha chiswe. Zulu zambiri za chiswe zimatalika mamita awiri kapena asanu kupita m'mwamba.
Chiswe chimagwira ntchito zosiyanasiyana m'gulu lawo. Gang'a ndi Teketeke ndi chiswe cha antchito. Ogwira ntchito onse ndi akazi. "Ndife omanga komanso mainjiniya!" akutero Gang'a.
Chiswe chogwira ntchito chimamanga ndi kusamalira chisa. Teketeke akuti, "Timamanga zisa zazikulu, komanso zovuta kumanga."
"Tiyeni tifotokoze mmene timamangira nyumba zathu," atero Gang'a. "Timayamba ndi kukumba njira zapansi panthaka."
Teketeke alowerera, "Timagwiritsa ntchito nsagwada zathu zamphamvu kukumba nthaka. Titha kusuntha dothi lambiri!"
"Kuti makoma a njira zathu akhale olimba, timawapaka malovu ndi dothi," akutero Teketeke.
"Zomatazo zikauma, zimalimba ngati dongo. Zisa za chiswe zimatha kukhala nthawi yayitali," awonjezera Gang'a.
"Timanyamula dothi lomwe timakumba ndikumangira chulu pamwamba pa nthaka. Chuluchi kawirikawiri chimakhala chozungulira, komanso ndi njira zambiri," atero Teketeke.
"Zulu zina zimatalika mamita asanu ndi anayi!" atero Gang'a.
Chiswe ndi tizirombo tokhala m'magulu akuluakulu. Chimakhala ndi maudindo osiyanasiyana popanga ndi kusamalira gululo.
Chiswe cha antchito monga Teketeke ndi Gang'a chimakumba ndi kumanga chisacho. Chiswe cha asilikali chimayang'anira chisa. Chiswe chogwira ntchito ndi cha asilikali chimapita kukafunafuna malo atsopano omangako zisa.
Chiswe cha namwino chimasamalira makechulu ndi ana achiswe.
Chisa chili ndi magawo osiyanasiyana. Muli zipinda za mfumukazi, zipinda za ana, ndi zipinda zosungiramo chakudya. Njira zimalumikiza madera osiyanasiyanawa.
Makechulu ndi chiswe chachikulu kwambiri ndipo chimatha kukhala ndi moyo wautali kuposa onse.
Teketeke akupitiriza kuti, "Timamanga njira mpaka pamwamba kuti mpweya wabwino uziyenda muchisa." Gang'a awonjezera kuti, "Chiswe chimafuna mpweya wabwino kuti chikhale ndi moyo."
Teketeke apitiliza kunena kuti, "Njirazi zimathandizanso kuti chisa chisamatenthe kwambiri."
"Tili ndi minda m'chisa chathu, momwe timalima bowa. Timasonkhanitsa tizidutswa ta zomera ndi zinthu zina zachilengedwe, zomwe timagwiritsa ntchito polima bowa," atero Teketeke.
"Kukomako!" abwekera Gang'a. "Minda ya bowa imadyetsa gulu lonse. Ndife mtundu wokhawo wa chiswe omwe timalima bowa."
Gulu lachiswe limakhala ndi makechulu ndi mfumu. Ogwira ntchitowa amadyetsa ndi kuteteza chiswe chofunikirachi.
Makechulu nthawi zambiri amakhala moyo zaka pakati pa 20 ndi 30. Amatha kuikira mazira mamiliyoni pa moyo wake. Ana amachoka ku mazira ndipo chiswe chaunamwino chimawasamalira.
Teketeke akuti, "Gulu lachiswe limakhala ladongosolo labwino kwambiri. Chiswe chilichonse chimathandizira kukhalapo ndi kukula kwa gulu lonse."
Gang'a akuwonjezera kuti, "Aliyense ali ndi ntchito yoti agwire, ndipo timaichita. Chiswe chimagwirira ntchito limodzi bwino." "Inde," akuvomereza motero Teketeke. "Tsopano tiyeni tibwerere kokumba!"

