

Anthu amakhala m'nyumba zosiyanasiyana. Nyumba zina zimamangidwa ndi zinthu za chilengedwe monga udzu. Nyumba zina zimamangidwa ndi zinthu zopangidwa ndi anthu, monga magalasi ndi konkireti.
Nyumba zina zimamangidwa ndi zinthu zachilengedwe komanso zopangidwa, monga nyumba ya ndendera m'nkhaniyi.
Kabo ndi Thabo amakhala m'boma la Katelera m'dziko la Botswana, pafupi ndi mudzi wa Mochudi. Amakhala m'nyumba ya ndendera ndi makolo awo.
"Nyumba ya ndendera ndi nyumba yozungulira ya chikhalidwe chamakolo yokhala ndi denga laudzu. Nyumbazi zimamangidwa m'madera ambiri kumwera kwa Africa," akufotokoza motero Kabo.
Thabo akupitiriza nati, "Nyumba za ndendera ndi zozungulira, zimakhala ndi khomo limodzi ndi mawindo. Masiku ano zikumakhala ndi mawindo agalasi, omwe kunalibe m'masiku akale."
"Agogo athu aamuna anamanga nyumbayi mwachikale. Bambo athu anawonjezera zinthu zina zamakono," akutero Kabo.
"Ndifotokoze mmene ntchito yomanga imayendera," atero Kabo.
Akupitiliza nati, "Omanga anagwiritsa ntchito matabwa, udzu, miyala, matope ndi pulasitala.
Iwo anayamba ndi kukumba dzenje. Amadzadzitsa dzenjelo ndi miyala ing'onoing'ono, dothi, ndi mchenga. Izi zimapanga maziko olimba oti amangepo."
Thabo akupitiriza nati, "Omanga amalowetsa mitengo yayitali pa mazikopo, kuzungulira m'mbalim'mbali. Amamanga mitengoyo kupanga mpanda wamitengo wa khoma lakunja kwa nyumbayo.
Atamaliza kumanga mitengoyo, omangawo amasomekamo miyala mothinana."
"Kenako, omangawo amasakaniza dongo, madzi, ndi ndowe za ng'ombe. Izi zimapanga dothi lachilengedwe lomwe limakhala lolimba kwambiri likauma. Amamata dothilo pakati pa miyalayo kuti igwirane," atero Kabo.
"Kumanga ndi miyala ndi matope kumapanga makoma olimba amene amakhala kwa nthawi yaitali," awonjezera motero Thabo.
Kabo akuti, "Makoma okhuthala akunja amakuta nyumba yathu."
Thabo akufotokoza kuti, "Izi zitanthauza kuti mkati mumakhala mozizira pamene kunja kukutentha. Kutentha kwa dzuwa sikungadutse makomawa.
M'malo ozizira kwambiri, kukutiraku kumachititsa kuti mkati muzitentha m'nyengo yozizira posunga kutentha mkati."
"Omanga nyumba ya ndendera yathu anaphamika matope m'maziko omwe adapanga," atero Thabo.
Kabo ati, "Kuti amalize pansi, anathira dothi lomaliza lonyowa kenako ndi kulitsendera. Dothili lidauma molimba ndipo zidachititsa kuti pansipo pakhale pofanana."
Thabo akuti, "Pomaliza amayika denga. Nyumba ya ndendera imakhala ndi denga losongoka la udzu.
Omanga analuka mitengo ndipo mitengo inakumana pakati pa dengalo. Analukira mitolo ya udzu kumitengoyo mosanjikana. Denga laudzu silidontha."
Udzu ndi ofunikira padenga. Koma udzu umenewu umakhalanso malo abwino okhalamo tizilombo ndi tinyama tina. Zambiri mwa izo ndi tizirombo towononga!
Yang'anani pa chithunzichi ndipo mupeze: akangaude atatu, chinkhanira, chikumbu, chiswe, ndi mbewa?
Zinthu zachilengedwe monga udzu wopangira denga zimakhala malo abwino akuti akangaude azikhalamo komanso kusaka.
Akangaude sawononga udzu ndipo amathandizira kuchepetsa tizilombo tina.
Tiyenera kusamalira udzu wadenga kuti tipewe tizirombo monga mbewa, utitiri, ndi chiswe.
"Timakhalamo ambiri mu nyumba ya ndenderayi!" akutero Thabo, akuyang'ana udzu. Akuopa akangaude.
"Ndimadabwa kuti ndi zolengedwa zina ziti zomwe zimatizungulira?" Adafunsa mwamantha Kabo.
"Ndikadzamanga nyumba ya ndendera yanga, idzakhala ndi denga la matailosi!" Kabo aseka.

