Timakhala m'nyumba zosanjikizana
Nina Orange
Kenneth Boyowa Okitikpi

Anthu amakhala m'nyumba zosiyanasiyana.
Ena amakhala m'nyumba za m'mwamba, mlengalenga. Ena amakhala m'nyumba za pansi.

Nyumba zitalizitali zimakhala ndi nyumba zina zambiri pamwamba pake. Nkhaniyi ikukhudza kumanga nyumba zosanjikizana zambirimbiri.

1

Misheli ndi Katalina ndi pachichemwali. Misheli watsala pang'ono kumaliza maphunziro ku sekondale. Katalina ali mkalasi yomaliza ku pulayimale sukulu.

Atsikanawa amakhala ndi makolo ndi agogo awo aakazi, m'nyumba yayitali mumzinda wa Nairobi. Amakonda kukhala m'mwamba mwa tawuni, ngati mbalame mumtengo.

2

Banjali limakhala m'nyumba ya nambala 22 kuchoka pansi. Amagwiritsa ntchito chikepe kuti akafike m'nyumba yawo.

Katalina amawerenga nyumba zosanjikizanazo pokwera ndi kutsika. Amafuna kudzakhala woyendetsa ndege. Misheli amafuna kudzakhala katswiri wa zomangamanga komaso kuti adzamange nyumba zosanjikizana.

3

Katalina afunsa, "Kodi nyumba yathuyi ndi yayitali kwambiri muAfrika muno?"

Misheli ayankha, "Ayi, nyumbayi ndi yotalika mamita 126. Nyumba yayitali kwambiri muAfrika ili ndi mamita 393, padziko lonse ili ndi mamita 830!"

"Eeeh! Nyumba zotalika chonchi zimaima bwanji?" Katalina adabwa.

4

"Nyumba zosanjikizana zonse zimamangidwa chimodzimodzi. Zomangira zofunikira kwambiri ndi zitsulo ndi konkireti.

Nyumbazi zimamangidwa imodziimodzi, kuyamba ndi zitsulo, kenako kuphatikiza konkireti muzitsulomo. Zimenezi kuziphatikiza zimalimba kwambiri ndipo zimakhala nthawi yayitali," ayankha Misheli.

5

Pomanga nyumba zosanjikizana, omanga amayenera kukumba dzenje lakuya kwambiri kuti likhale maziko.

Chimodzimodzi mtengo wautali umakhala ndi mitsitsi ikuluikulu, yakuya, nyumba zosanjikizana zimayenera kukhala ndi maziko olimba pathanthwe. Nthawi zina thanthwe limakhala pansi m'nthaka.

6

Kenako, omanga amayenera kumanga zam'mbalim'mbali za nyumba. Zam'mbalizi amamangira zitsulo zitalizitali.

Zitsulozi zimathandiza kumanga nyumba zitalizitali. Zitsulo zimatha kunyamula zinthu zolemera kwambiri.

Zam'mbalim'mbali za zitsulozi ndi mtima wa nyumba, ngati mafupa a munthu.

7

Zitsulo zimatha kupindika. Izi zitanthauza kuti nyumba itha kutepa pang'ono (ngakhale kuti izi sizingaoneke).

Kukakhala mphepo yamphamvu, kapena chivomerezi, zitsulo zimachititsa nyumba ija kutepa pang'ono.

Zitsulo zimakhala zolimbitsa nyumba komanso zotepa.

8

Zomangira zina ndi konkireti. Konkireti ndi kasakaniza wa mchenga, simenti, ndi madzi. Omanga amaphatikiza konkireti kuti apange chiphalaphala cholimba, chimene amathira muzitsulo zolukana.

Konkireti ikaikidwa, imalimba ngati thanthwe. Izi zimapanga pansi ndi makoma a nyumba.

9

Amamanga nyumbazi kuyambira pansi, imodzi imodzi. Nyumba zapansi zimasenza kulemera kwakukulu. Konkireti imatha kusenza kulemera kuteroko, kuchititsa nyumba kukhala yolimba ndi kukhazikika.

Konkireti imazungulira zitsulo zolukidwa, kuteteza zitsulo ku madzi ndi mphepo (Madzi ndi m'pweya zimayambitsa dzimbiri).

10

Njira zoyendamo chikepe zimamangidwanso nthawi yomweyi. Kumanga zitsulo ndi konkireti kukatha, omanga amaika mawindo. Kenako amaika siling'i, makoma, ndi kumalizitsa pansi.

Nyumba imafuna kulumukiza mawaya a magetsi ndi mapaipi oyendamo madzi ndi otayira zoipa.

11

Pomaliza, omanga amaika magetsi, zitseko, makabati ndi zina zofunikira pokhala ndi kumanga nyumba zosanjikizana.

Misheli ati, "Matauni akuluakulu ambiri malo akuwathera. Nyumba zosanjikizana zimagwiritsa ntchito bwino malo. Ndikadzakhala katswiri wa zomangamanga, ndidzathandizira kumanga nyumba yayitali kwambiri padziko lapansi!"

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Timakhala m'nyumba zosanjikizana
Author - Nina Orange, Ursula Nafula
Translation - Peter Msaka
Illustration - Kenneth Boyowa Okitikpi
Language - ChiChewa
Level - Read aloud