

Kunali mtsikana wina wokongola.
Tsiku lina, anali ndi njala kwambiri. Anaganiza za njira yopezera chakuti adye.
Anakumana ndi bambo yemwe anamufunsa, "Ulibwanji mtsikana? Chakukwiyitsa ndi chiyani?"
Mtsikanayu anayankha, "Ndili ndi njala."
Bamboyo anamumvera chisoni mtsikanayu. Anamuuza kuti munali phwando m'mudzimo ndipo apite kumeneko akabe chakudya.
Mtsikanayu anali asanabepo ndi kale lonse.
Iye anadzuka mwachangu ndi kupita ku nyumba komwe kumachitikira phwandolo.
Atayandikira, anayiwala malangizo obera aja. Anayimba mobwerezabwereza:
Ndabwera kudzaba chakudya, cha-ku-dya,
ndikuyenda pang'onopang'ono, pang'onopang'ono.
Anthu anayamba kumva nyimbo ya mtsikanayo ali patali mpaka anafika pa malo aphwandowo.
Anthu anali odabwa ndi mtundu wa nyimboyo ndipo anamufunsa, "Ukuchokera kuti? Ukufuna chiyani? N'chifukwa chani ukuyimba?"
Mtsikanayu anawauza kuti anali ndi njala ndipo anamupatsa chakudya.
Kenako, analangizidwa kuti kuba ndi koyipa.

