

Mbuzi inali mfumu ya nyama ndi mbalame zonse.
Inayitanitsa msonkhano.
Mbuzi inawauza kuti inalota maloto.
Onse anamvetsera.
Maloto anali okhudzana ndi njala.
"Ndiye titani?" anafunsa Mphaka.
Nkhuku ndi Bakha adati, "Tisunge chakudya m'nkhokwe ya mfumu."
Mfumu Mbuzi inati, "M'mangeni aliyense amene samvera."
Nthawi inakwana yosankha mfumu ina.
Anasankha Mphaka.
Mbuzi siinafune Mphaka akhale mfumu.
"Mfumu ndine," Mbuzi inatero mokwiya.
Mbuzi siinadye chakudya.
Ng'ombe inafunsa, "Titani?"
Nyamazo ndi mbalame zinakambirana.
Zinakwiya ndi khalidwe la Mbuzi.
Galu anati, "Ndinali naye m'mene anali mfumu."
Nkhosa inati, "Ndimapatsa ana ake bweya wanga wokongola mmene anali mfumu."
Nkhumba inati, "Ali mfumu, ndimasamala munda wake?"
"Kodi Mbuzi inaganiza kuti idzakhala mfumu mpaka muyaya?" Nkhosa inafunsa.
Nyama zinagwirizana kuti Mbuzi asamutsire chakudya kwa mfumu Mphaka.
Nyama zindapeza Mbuzi ikupuma.
Mbuzi inati, "Ndidzakhala mfumu ya muyaya."
"Tikumanga ndikukutengera kwa mfumu yatsopano."
Ng'ombe inakokera mbuzi ku bwalo la mfumu.
Nyama zina zinachemerera.
N'chifukwa chake mbuzi zimakana kuyenda, zikamakokedwa.

