Ndalama zili m'mabuku
Abraham Bereket
Adonay Gebru

M'mudzi wina munali mnyamata yemwe dzina lake linali Chavuta.

Samakonda kuwerenga ngakhale kutsekula buku kumene. Anali mwana wa ulesi. Analinso ndi khalidwe loyipa.

1

Chavuta amaba ndalama za amayi ake kukagulira maswiti. Ngakhale amayi ake abise ndalama zawo, iye anali kuzipeza ndikuzitenga.

Akatha kudya maswiti ake, Chavuta amakasewera ndi anzake.

2

Patapita masiku, Chavuta anasiya kupita ku sukulu. Amakhalira kusewera tsiku lonse, ndi kubwelera kunyumba madzulo.

Amayi ake anadziwa izi ndipo anali wodandaula.

3

"Mwana wathu alibe khalidwe. Ndikuganiza kuti sakupitanso ku sukulu. Akundibera ndalama," anatero mayi ake a Chavuta.

4

Bambo aja anati, "Ulendo wina, mudzabise ndalama mkati mwa buku. Satsekula buku olo limodzi. Ndiye ndalama zanu zidzatetezeka m'menemo."

5

Tsiku lotsatiralo, Chavuta anafunafuna ndalama za amayi ake koma sanapeze kalikonse.

Anaganiza zopita pa msika wapafupi kukasaka ndalama.

6

Bambo ake anaona komwe Chavuta amapita.

"Mwana wanga, ndikudziwa chifukwa chomwe ukupitira ku msika. Tsopano pitanso m'nyumba ndipo ukafune ndalama m'mabuku," anatero bamboyo.

7

Chavuta anali wodabwa, koma anabwelera kukafuna ndalama m'mabuku muja.

Anapeza ndalama zomwe mayi ake anabisa.

8

Tsiku lotsatiralo, anayang'ananso m'mabuku koma sanapeze kalikonse.

Anapita kwa bambo ake kukafunsa kuti chifukwa chiyani munalibe ndalama m'mabukumo.

9

Bambo ake anamwetulira ndi kumuyankha, "Mwana wanga, ukufuna ndalama zokwana kugula maswiti ambiri?"

Chavuta anayankha, "Inde bambo."

10

Bambo ake anati, "Mvetsera mosamala. Uziwerenga mabuku ako komanso kumalowa mkalasi. Udzapeza phindu m'mabuku. Osafooka."

"Koma bambo, kuwerenga ndi kotopetsa. Mabuku ndi ogwetsa ulesi!" Chavuta anayankha.

11

Kwa kanthawi, bambo ake a Chavuta anakhala chete. Anaganiza m'mene akanamulimbikitsira mwana wawoyo.

Kenako anati, "Tiye tiziwerenga limodzi. Ndikuthandiza kupeza chuma m'mabuku."

12
You are free to download, copy, translate or adapt this story and use the illustrations as long as you attribute in the following way:
Ndalama zili m'mabuku
Author - Abraham Bereket, Hardido Temesgen, Yohannes Firew
Translation - Peter Msaka
Illustration - Adonay Gebru
Language - ChiChewa
Level - Longer paragraphs